1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,
2 Imvani mau a pangano ili, nenani kwa anthu a Yuda, ndi anthu a Yerusalemu;
3 ndi kunena kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Aisrayeli: Wotembereredwa ndi munthu wosamvera mau a pangano ili,
4 limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, m'ng'anjo ya citsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwacita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu;
5 kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko mayenda mkaka ndi uci, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.
6 Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau onsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwacita.
7 Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawaturutsa iwo ku dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.
8 Koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; cifukwa cace ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti acite, koma sanacita.
9 Ndipo Yehova anati kwa ine, Ciwembu caoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala m'Yerusalemu.
10 Abwerera kucitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu yina kuti aitumikire; nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.
11 Cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo coipa, cimene sangathe kucipulumuka; ndipo adzandipfuulira Ine, koma sindidzamvera iwo.
12 Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzapfuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.
13 Pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira camanyazi, alingana ndi kucuruka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.
14 Cifukwa cace usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andipfuulira Ine m'kusaukakwao.
15 Wokondedwa wanga afunanji m'nyumba mwanga, popeza wacita coipa ndi ambiri, ndipo thupi lopatulika lakucokera iwe? pamene ucita coipa ukondwera naco.
16 Yehova anacha dzina lako, Mtengo waazitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikuru wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zace zatyoka.
17 Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe coipa, cifukwa ca zoipa za nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzicitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.
18 Ndipo Yehova anandidziwitsa, ndipo ndinadziwa; ndipo wandisonyeza ine macitidwe ao.
19 Koma ine ndinanga mwana wa nkhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwa kuti anandicitira ine ciwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zace, timdule iye pa dziko la amoyo, kuti dzina lace lisakumbukikenso.
20 Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, pamene ayesa imso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera cilango, pakuti kwa Inu ndaulula mlandu wanga.
21 Cifukwa cace atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu;
22 cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao amuna ndi akazi adzafa ndi njala;
23 ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera coipa pa anthu a ku Anatoti, caka ca kulangidwa kwao.