1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,
2 Tauka, tatsikira ku nyumba ya woumba, pamenepo ndidzakumvetsa mau anga.
3 Ndipo ndinatsikira ku nyumba ya woumba, ndipo, taonani, anaumba nchito yace ndi njinga.
4 Ndipo pamene mbiya alikulumba ndi dothi inaonongeka m'dzanja la woumba, anaiumbanso mbiya yina, monga kunamkomera woumba kulumba.
5 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
6 Nyumba ya Israyeli inu, kodi sindingathe kucita ndi inu monga woumba uyu? ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israyeli.
7 Mphindi imene ndidzanena za mtundu wa anthu, kapena za ufumu, kuti ndizule ndi kupasula ndi kuononga;
8 ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka coipa cao, ndidzaleka coipaco ndidati ndiwacitire.
9 Ndipo mphindi imene ndikanenera mtundu, ndi ufumu, kuti ndimangitse mudzi wace ndi kuuoka;
10 koma ukacita coipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka cabwinoco, ndidati ndiwacitire.
11 Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu coipa, ndilingalira inu kanthu kakucitira inu coipa; mubwerere tsono inu nonse, yense ku njira yace yoipa, nimukonze njira zanu ndi macitidwe anu.
12 Koma iwo ati, Palibe ciyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzacita yense monga mwa kuuma kwa mtima wacewoipa.
13 Cifukwa cace atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israyeli wacita cinthu coopsetsa kwambiri.
14 Kodi matalala a Lebano adzalephera pa mwala wa m'munda? kodi adzaphwa madzi ozizira otsika kutari?
15 Pakun anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pace; apunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;
16 kuti aliyese dziko lao likhale lodabwitsa, ndi: kutsonya citsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wace.
17 Ndidzamwazamwaza iwo monga ndi mphepo ya kum'mawa pamaso pa adani; ndidzayang'anira pamsana pao, si nkhope yao, tsiku la tsoka lao.
18 Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya comcitira coipa; pakuti cilamulo sicidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ace ali onse.
19 Mundimvere ine, Yehova, mumve mau a iwo akulimbana ndi ine.
20 Kodi coipa cibwezedwe pa cabwino? pakuti akumbira moyo wanga dzenje, Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwacotsera iwo ukali wanu.
21 Cifukwa cace mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo ku mphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.
22 Mpfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.
23 Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize cimo lao pamaso panu; apunthwitsidwe pamaso panu; mucite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.