Yeremiya 23 BL92

Mau akutsutsa abusa osakhulupirika

1 Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! ati Yehova.

2 Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipitikitsa, ndipo simunazizonda; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa nchito zanu, ati Yehova.

3 Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m'maiko onse m'mene ndinazipitikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso ku makola ao; ndipo zidzabalana ndi kucuruka.

4 Ndipo ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhawa, sipadzasowa mmodzi yense, ati Yehova.

Mphukira wa Davide

5 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzacita mwanzeru, nadzacita ciweruzo ndi cilungamo m'dziko lino.

6 Masiku ace Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israyeli adzakhala mokhazikika, dzina lace adzachedwa nalo, ndilo Yehova ndiye cilungamo cathu.

7 Cifukwa cace, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto;

8 koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israyeli kuwaturutsa m'dziko la kumpoto, ndi ku maiko onse kumene ndinawapitikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao.

Mau akutsutsa aneneri onama

9 Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; cifukwa ca Yehova, ndi cifukwa ca mau ace opatulika.

10 Pakuti dziko ladzala ndi acigololo; pakuti cifukwa ca temberero dziko lilira, mabusa a kucipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siiri yabwino.

11 Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.

12 Cifukwa cace njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzacotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.

13 Ndipo ndinaona kupusa mwa aneneri a ku Samariya; anenera za Baala, nasokeretsa anthu anga Israyeli.

14 Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona cinthu coopsetsa; acita cigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ocita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zace; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ace ngati Gomora.

15 Cifukwa cace Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo cowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwaturukira kunka ku dziko lonse.

16 Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zacabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.

17 Anena cinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wace amati, Palibe coipa cidzagwera inu.

18 Pakuti ndani waima m'upo wa Yehova, kuti aone namve mau ace? ndani wazindikira mau anga, nawamva?

19 Taonani, cimphepo ca Yehova, kupsa mtima kwace, kwaturuka, inde cimphepo cozungulira; cidzagwa pamutu pa woipa.

20 Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atacita, mpaka atatha maganizo a mtima wace; masiku otsiriza mudzacidziwa bwino.

21 Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanena ndi iwo, koma ananenera.

22 Koma akadaima m'upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo ku njira yao yoipa, ndi ku coipa ca nchito zao.

23 Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patari?

24 Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? ati Yehova.

25 Ndamva conena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.

26 Ici cidzakhala masiku angati m'mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a cinyengo ca mtima wao?

27 amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wace, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimcha nalo Baala.

28 Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lace; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi ciani polinganiza ndi tirigu? ati Yehova.

29 Kodi mau anga safanafana ndi moto? ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?

30 Cifukwa cace, taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene amaba mau anga, yense kumbera mnansi wace.

31 Taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene acita ndi malilime ao, ndi kuti, Ati Iye.

32 Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao acabe; koma Ine sindinatuma iwo, sindinauza iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.

33 Ndipo pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndi ciani? pamenepo uziti kwa iwo, Katundu wanji? Ndidzakucotsani inu, ati Yehova.

34 Koma za mneneri, ndi wansembe, ndi anthu, amene adzati, Katundu wa Yehova, ndidzamlanga munthuyo ndi nyumba yace.

35 Mudzatero yense kwa mnansi wace, ndi yense kwa mbale wace, Yehova wayankha ciani? ndipo Yehova wanena ciani?

36 Ndipo katundu wa Yehova simudzachulanso konse; pakuti mau a munthu adzakhala katundu wace; pakuti mwasokoneza mau a Mulungu wamoyo, Yehova wa makamu, Mulungu wathu.

37 Uzitero kwa mneneri, Yehova wakuyankha ciani? ndipo Yehova wanenanji?

38 Koma ngati muti, Katundu wa Yehova, cifukwa cace Yehova atero: Cifukwa muti mau awa, Katundu wa Yehova, ndipo ndatuma kwa inu, kuti, Musati, Katundu wa Yehova;

39 cifukwa cace, taonani, ndidzakuiwalani inu konse, ndipo ndidzakucotsani, ndi mudzi umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, ndidzaucotsa pamaso panga;

40 ndipo ndidzakutengerani inu citonzo camuyaya, ndi manyazi amuyaya, amene sadzaiwalika.