Yeremiya 44 BL92

Acenjeza mowaopsa Ayuda amene adathawira ku Aigupto

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Aigupto, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti,

2 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Mwaona coipa conse cimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa midzi yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe iri bwinja, palibe munthu wokhalamo;

3 cifukwa ca coipa cao anacicita kuutsa naco mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu yina, Imene sanaidziwa, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.

4 Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musacitetu conyansa ici ndidana naco.

5 Koma sanamvera, sanachera khutu lao kuti atembenuke asiye coipa cao, osafukizira milungu yina.

6 Cifukwa cace mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.

7 Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Cifukwa canji mucitira miyoyo yanu coipa ici, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;

8 popeza muutsa mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu, pofukizira milungu yina m'dziko la Aigupto, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale citemberero ndi citonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi?

9 Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazicita m'dziko la Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu?

10 Sanadzicepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'cilamulo canga, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.

11 Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikucitireni inu coipa, ndidule Yuda lonse.

12 Ndipo ndidzatengaotsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Aigupto akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Aigupto adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkuru, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo.

13 Ndipo ndidzalanga iwo okhala m'dziko la Aigupto, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi caola;

14 kuti otsala a Yuda, amene ananka ku dziko la Aigupto kukhala m'menemo, asapulumuke asatsale ndi mmodzi yense, kuti abwere ku dziko la Yuda, kumene afuna kubwera kuti akhale m'menemo; pakuti adzabwera koma adzapulumuka ndiwo.

15 Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu yina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukuru, anthu onse okhala m'dziko la Aigupto, m'Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti,

16 Koma mau amene wanena ndi ife m'dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe.

17 Koma tidzacita ndithu mau onse anaturuka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tikacitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akuru athu, m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi cakudya cokwanira, tinakhala bwino, sitinaona coipa.

18 Koma cilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi caola.

19 Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu?

20 Ndipo Yeremiya anati kwa anthu onse, kwa amuna, ndi kwa akazi, kwa anthu onse amene anambwezera mau amenewa, ndi kuti,

21 Zofukizira zanu m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akuru anu, ndi anthu a m'dziko, kodi Yehova sanazikumbukira, kodi sizinalowa m'mtima mwace?

22 ndipo Yehova sanatha kupirirabe, cifukwa ca macitidwe anu oipa, ndi cifukwa ca zonyansa zimene munazicita; cifukwa cace dziko lanu likhala bwinja, ndi cizizwitso, ndi citemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.

23 Cifukwa mwafukiza, ndi cifukwa mwacimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'cilamulo cace, ndi m'malemba ace, ndi m'mboni zace, cifukwa cace coipaci cakugwerani, monga lero lomwe.

24 Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m'dziko la Aigupto.

25 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m'kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzacita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, citani zowinda zanu.

26 Cifukwa cace tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Aigupto: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikuru, ati Yehova, kuti dzina langa silidzachulidwanso m'kamwa mwa munthu ali yense wa Yuda m'dziko la Aigupto, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.

27 Taonani, ndiwayang'anira kuwacitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Aigupto adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.

28 Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kuturuka ku dziko la Aigupto kulowa m'dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m'dziko la Aigupto kuti akhale m'menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao.

29 Ndipo ici cidzakhala cizindikiro ca kwa inu, ati Yehova, cakuti Ine ndidzakulangani m'malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akucitireni inu zoipa.

30 Yehova atero: Taonani, ndidzapereka Farao Hofra mfumu ya Aigupto m'manja a adani ace, ndi m'manja a iwo akufuna moyo wace; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m'manja a Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo mdani wace, amene anafuna moyo wace.