Yeremiya 31 BL92

Mwa cikondi ca Mulungu adzabweza Israyeli

1 Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israyeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.

2 Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza cisomo m'cipululu; Israyeli, muja anakapuma.

3 Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi cikondi cosatha; cifukwa cace ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.

4 Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israyeli; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzaturukira masewero a iwo akukondwerera.

5 Ndiponso udzalima minda ya mphesa pa mapiri a Samariya; akunka adzanka, nadzayesa zipatso zace zosapatulidwa.

6 Pakuti lidzafika tsiku, limene alonda a pa mapiri a Efraimu adzapfuula, Ukani inu, tikwere ku Ziyoni kwa Yehova Mulungu wathu.

7 Pakuti Yehova atero, Yimbirirani Yakobo ndi kukondwa, pfuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israyeli,

8 Taonani, ndidzatenga iwo ku dziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikuru lidzabwera kuno.

9 Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa ku mitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzapunthwa, pakuti ndiri Atate wace wa Israyeli, ndipo Efraimu ali mwana wanga woyamba.

10 Tamvani mau a Yehova, amitundu inu, lalikirani m'zisumbu zakutari; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israyeli adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa acita ndi zoweta zace.

11 Pakuti Yehova wapulumutsa Yakobo, namuombola iye m'dzanja la iye amene anamposa mphamvu,

12 Ndipo adzadza nadzayimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira, ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikuru; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamicera; ndipo, sadzakhalanso konse ndi cisoni.

13 Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye cisoni cao.

14 Ndipo ndikhutitsa moyo wa ansembe ndi mafuta, ndipo anthu anga adzakhuta ndi zokoma zanga, ati Yehova.

Rakeli adzatonthozedwa

15 Atero Yehova: Mau amveka m'Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakeli alinkulirira ana ace; akana kutonthozedwa mtima pa ana ace, cifukwa palibe iwo.

16 Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti nchito yako idzalandira mphoto, ati Yehova; ndipo adzabweranso kucokera ku dziko la mdani.

17 Ndipo ciripo ciyembekezero ca citsirizo cako, ati Yehova; ndipo ana ako adzafikanso ku malire ao.

18 Kumva ndamva Efraimu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwana wa ng'ombe wosazolowera gori; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.

19 Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ncafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, cifukwa ndinasenza citonzo ca ubwana wanga.

20 Kodi Efraimu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; cifukwa cace mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamcitiradi cifundo, ati Yehova.

Aisrayeli adzakhalanso bwino m'dziko mwao

21 Taimitsa zizindikiro, udzipangire zosonyeza; taika mtima wako kuyang'anira mseu wounda, njira imene unapitamo; tatembenukanso, iwe namwali wa Israyeli, tatembenukiranso ku midzi yako iyi.

22 Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati; iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? pakuti Yehova walenga catsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.

23 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'midzi yace, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo cilungamo, iwe phiri lopatulika.

24 Ndipo Yuda ndi midzi yace yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.

25 Pakuti ndakhutidwa mtima wolema, ndadzazanso mtima uli wonse wacisoni.

26 Pamenepo ndinauka, ndinaona; ndipo tulo tanga tinandizunira ine.

27 Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.

28 Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzyala, ati Yehova.

29 Masiku omwewo sadzanenanso, Atate adya mphesa zowawa, ndi mano a ana ayayamira.

30 Koma yense adzafa cifukwa ca mphulupulu yace; yense amene adya mphesa zowawa, mano ace adzayayamira.

Pangano latsopano pakati pa Mulungu ndi anthu ace

31 Taonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya lsrayeli, ndi nyumba ya Yuda;

32 si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.

33 Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika cilamulo canga m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzacilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;

34 ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wace, ndi yense mbale wace, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira cimo lao.

35 Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ace agabvira; Yehova wa makamu ndi dzina lace:

36 Ngati malembawa acoka pamaso panga, ati Yehova, pamenepo mbeunso ya Israyeli idzaleka kukhala mtundu pamaso panga ku nthawi zonse.

37 Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzacotsa mbeu zonse za Israyeli cifukwa ca zonse anazicita, ati Yehova.

38 Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mudziwu udzamangidwira Yehova kuyambira pa nsanja ya Hananeli kufikira ku cipata ca kungondya.

39 Ndipo cingwe coyesera cidzaturukanso kulunjika ku citunda ca Garebi, ndipo cidzazungulira kunka ku Goa.

40 Ndipo cigwa conse ca mitembo, ndi ca phulusa, ndi minda yonse: kufikira ku mtsinje wa Kidroni, kufikira kungondya kwa cipata ca akavalo kuloza kum'mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse ku nthawi zamuyaya.