Yeremiya 33 BL92

Yehova abwereza kunena kuti anthu ace adzakhazikikanso m'dziko mwao, padzakhalanso mphukira

1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya nthawi yaciwiri, pamene iye anali citsekedwere m'bwalo la kaidi, kuti,

2 Atero Yehova wocita zace, Yehova wolenga zace kuti azikhazikitse; dzina lace ndi Yehova:

3 Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikuru, ndi zolakika, zimene suzidziwa.

4 Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za nyumba za mudzi uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda'zi, zinagwetsedwa ziwacinjirizire mitumbira, ndi lupanga:

5 Adza kumenyana ndi Akasidi, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mudzi uno nkhope yanga cifukwa ca zoipa zao zonse.

6 Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuciritsa, ndi kuwaciritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kucuruka kwa mtendere ndi zoona.

7 Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israyeli, ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, monga poyamba paja,

8 Ndipo ndidzawayeretsa kucotsa mphulupulu yao, imene anandicimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandicimwira, nandilakwira Ine.

9 Ndipo ndidzayesa mudzi uno cifukwa ca kukondwa, ndi ciyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a pa dziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawacitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira cifukwa ca zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzaucitira.

10 Atero Yehova: M'malo muno, m'mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m'midzi ya Yuda, m'makwalala a Yerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,

11 mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, cifundo cace ncosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.

12 Yehova wa makamu atero: M'malo muno, muli bwinja, mopanda munthu ndi nyama, m'midzi yace yonse, mudzakhalanso mokhalamo abusa ogonetsa zoweta zao.

13 M'midzi ya kumtunda, m'midzi ya kucidikha, m'midzi ya ku Mwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'midzi ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.

14 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzakhazikitsa mau abwino aja ndinanena za nyumba ya Israyeli ndi za nyumba ya Yuda.

15 Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukitsira Davide mphukira ya cilungamo; ndipo adzacita ciweruzo ndi cilungamo m'dzikomu.

16 Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzachedwa nalo, Yehova ndiye cilungamo cathu.

17 Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wacifumu wa nyumba ya Israyeli;

18 ndiponso ansembe sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakucita nsembe masiku onse.

19 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

20 Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku m'nyengo yao;

21 pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wace; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.

22 Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mcenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; comweco ndidzacurukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.

23 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

24 Kodi sulingalira comwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? comweco anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.

25 Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;

26 pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zace kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isake, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweundende wao, ndipo ndidzawacitira cifundo.