1 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza cimodzi pamene analowa ufumu wace; ndipo analamulira m'Yerusalemu zaka khumi kudza cimodzi; dzina la amace ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina.
2 Ndipo iye anacita zoipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse anazicita Yehoyakimu.
3 Pakuti zonse zinacitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda cifukwa ca mkwiyo wa Yehova, mpaka anawacotsa pamaso pace; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babulo.
4 Ndipo panaoneka caka cacisanu ndi cinai ca ufumu wace mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anafika, iye ndi nkhondo yace, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zitando; ndipo anammangira malinga pozungulira pace.
5 Ndipo mudzi unazingidwa mpaka caka ca khumi ndi cimodzi ca mfumu Zedekiya.
6 Mwezi wacinai, tsiku lacisanu ndi cinai la mwezi, njala inabvuta m'mudzi, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya.
7 Pamenepo anaboola mudzi, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, naturuka m'mudzi usiku pa njira ya kucipata ca pakati pa makoma awiri, imene inali pa munda wa mfumu; Akasidi alikumenyana ndi mudzi pozungulira pace, ndipo anapita njira ya kucidikha.
8 Koma nkhondo ya Akasidi inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m'zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yace yonse inambalalikira iye.
9 Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babulo ku Ribila m'dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza.
10 Ndipo mfumu ya ku Babulo inapha ana a Zedekiya pamaso pace; niphanso akuru onse a Yuda m'Ribila.
11 Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, ndipo mfumu ya ku Babulo inammanga m'zigologolo, nimtengera ku Babulo, nimuika m'ndende mpaka tsiku la kufa kwace.
12 Mwezi wacisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndico caka cakhumi ndi cisanu ndi cinai ca Nebukadirezara, mfumu ya ku Babulo, analowa m'Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babulo:
13 ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za m'Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikuru zonse, anazitentha ndi moto.
14 Ndipo nkhondo yonse ya Akasidi, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pace.
15 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mudzi, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babulo, ndi otsala a unyinjiwo.
16 Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda.
17 Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Akasidi anazityolatyola, nanka nao mkuwa wace wonse ku Babulo.
18 Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazicotsa.
19 Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikapo nyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golidi, wa zija zagolidi, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazicotsa.
20 Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomo anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanatha kuyesa kulemera kwace.
21 Koma nsanamirazo, utari wace wa nsanamira yina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi cingwe ca mikono khumi ndi iwiri cinaizinga; kucindikira kwace kunali zala zinai; inali yagweregwere.
22 Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pace; utari wace wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi made ndi makangaza pakorona pozungulira pace, onse amkuwa: nsanamira inzace yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.
23 Ndipo pambali pace panali makangaza makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi limodzi; ndipo makangaza onse anali zana limodzi pamade pozungulira pace.
24 Ndipo kapitao wa alonda anatenga Seraya mkuru wansembe, ndi Zefaniya wansembe waciwiri, ndi akudikira pakhomo atatu;
25 ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makumi asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi.
26 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga iwo, nadza nao kwa mfumu ya ku Babulo ku Ribila.
27 Ndipo mfumu ya ku Babulo anawakantha, nawapha pa Ribila m'dziko la Hamati. Comweco Yuda anatengedwa ndende kuturuka m'dziko lace.
28 Amenewa ndi anthu amene Nebukadirezara anatenga ndende: caka cacisanu ndi ciwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu;
29 caka cakhumi ndi cisanu ndi citatu ca Nebukadirezara iye anatenga ndende kucokera m'Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri;
30 caka ca makumi awiri ndi zitatu ca Nebukadirezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.
31 Ndipo panali caka ca makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri ca undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babulo anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namturutsa iye m'ndende;
32 nanena naye bwino, naika mpando wace upose mipando ya mafumu amene anali naye m'Babulo.
33 Ndipo anapindula zobvala zace za m'ndende, ndipo sanaleka kudya pamaso pace masiku onse a moyo wace.
34 Koma phoso lace mfumu ya ku Babulo sanaleka kumpatsa, phoso tsiku ndi tsiku gawo lace, mpaka tsiku la kufa kwace, masiku onse a moyo wace.