Yeremiya 42 BL92

Yeremiya acenjeza anthu asapite ku Aigupto

1 Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi Jezaniya mwana wace wa Hosiya, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono, kufikira wamkuru, anayandikira,

2 nati kwa Yeremiya mneneri, Cipembedzero cathu cigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, cifukwa ca otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;

3 kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi comwe ticite.

4 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti ciri conse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.

5 Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati siticita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.

6 Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.

7 Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya.

8 Ndipo anaitana Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru,

9 nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pace,

10 Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa naco cisoni coipa cimene ndakucitirani inu.

11 Musaope mfumu ya ku Babulo, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndiri ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lace.

12 Ndipo ndidzakucitirani inu cifundo, li kuti iye akucitireni inu cifundo, nakubwezereni inu ku dziko lanu.

13 Koma mukati, Sitidzakhala m'dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu;

14 ndi kuti, Iai; tidzanka ku Aigupto, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;

15 cifukwa cace mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Aigupto, kukakhala m'menemo;

16 pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Aigupto, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Aigupto; pamenepo mudzafa.

17 Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Aigupto kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku coipa cimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.

18 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Aigupto; ndipo mudzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo; ndipo simudzaonanso malo ano.

19 Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe m'Aigupto; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.

20 Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzacita.

21 Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamva mau a Yehova Mulungu wanu m'cinthu ciri conse cimene Iye wanditumira ine naco kwa inu.

22 Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi caola, komwe mufuna kukakhalako.