1 Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panadza mau awa ocokera kwa Yehova, kuti,
2 Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa midzi yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.
3 Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yace yoipa; kuti ndileke coipa, cimene ndinati ndiwacitire cifukwa ca kuipa kwa nchito zao.
4 Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'cilamulo canga, cimene ndaciika pamaso panu,
5 kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvera;
6 pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mudzi uwu citemberero ca kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.
7 Ndipo ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya alinkunena mau awa m'nyumba ya Yehova.
8 Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.
9 Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mudzi uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.
10 Ndipo pamene akuru a Yuda anamva zimenezi, anakwera kuturuka ku nyumba ya mfumu kunka ku nyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la cipata catsopano ca nyumba ya Yehova.
11 Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akuru ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mudzi uwu monga mwamva ndi makutu anu.
12 Pamenepo Yeremiya ananena kwa akuru onse ndi kwa anthu onse, kuti, Yehova anandituma ine ndinenere nyumba iyi ndi mudzi uwu mau onse amene mwamva.
13 Cifukwa cace tsopano konzani njira zanu ndi macitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka coipa cimene ananenera inu.
14 Koma ine, taonani, ndiri m'manja anu; mundicitire ine monga mokomera ndi moyenera m'maso anu.
15 Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosacimwa, ndi pa mudzi uwu, ndi pa okhalamo ace; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu.
16 Pamenepo akuru ndi anthu onse anati kwa ansembe ndi kwa aneneri, Munthu uyu sayenera kufa: pakuti watinenera ife m'dzina la Yehova Mulungu wathu.
17 Ndipo anauka akuru ena a m'dziko, nati kwa msonkhano wa anthu, kuti,
18 Mika Mmorasi ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.
19 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? kodi sanamuopa Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka coipa cimene ananenera iwo? Cotero tidzaicitira miyoyo yathu coipa cacikuru.
20 Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wace wa Semaya wa ku Kiriati Yearimu; ndipo iye ananenera mudzi uwu ndi dziko lino monga mwa mau lonse a Yeremiya;
21 ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ace onse, ndi akuru onse, anamva mau ace, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Aigupto;
22 ndipo Yehoyakimu mfumu anatuma anthu ku Aigupto, Elinatanu mwana wace wa Akibori, ndi anthu ena pamodzi ndi iye, anke ku Aigupto;
23 ndipo anamturutsa Uriya m'Aigupto, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wace m'manda a anthu acabe.
24 Koma dzanja la Ahikamu mwana wa Safani linali ndi Yeremiya, kuti asampereke m'manja a anthu kuti amuphe.