Yeremiya 6 BL92

Acenjezedwa kuti adani adzamangira Yerusalemu misasa

1 Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga m'Tekoa, kwezani cizindikiro m'Beti-hakeremu; pakuti caoneka coipa coturuka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.

2 Ndidzacotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka.

3 Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pace.

4 Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka.

5 Ukani, tiyende usiku, tipasule nyumba zace.

6 Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mudzi wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwace modzala nsautso.

7 Monga kasupe aturutsa madzi ace, camweco aturutsa zoipa zace; ciwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwace; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.

8 Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakucokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.

9 Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israyeli monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakuchera mphesa m'mitanga yace.

10 Ndidzanena ndi yani, ndidzacita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao liri losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.

11 Cifukwa cace ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wace adzatengedwa, okalamba ndi iye amene acuruka masiku ace.

12 Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.

13 Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita monyenga,

14 Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.

15 Kodi anakhala ndi manyazi pamene anacita conyansa? lai, sanakhala konse ndi manyazi, sanathe kunyala; cifukwa cace adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika cwa iwo, aclzagwetsedwa, ati Yehova.

16 Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.

17 Ndipo ndinaika alonda oyang'anira inu, ndi kuti, Mverani mau a lipenga; koma anati, Sitidzamvera.

18 Cifukwa cace tamverani, amitundu inu, dziwani, msonkhano inu, cimene ciri mwa iwo.

19 Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera coipa pa anthu awa, cipatso ca maganizo ao, pakuti sanamvera mau anga, kapena cilamulo canga, koma wacikana.

20 Cofukiza cindifumiranji ku Seba, ndi nzimbe ku dziko lakutari? nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.

21 Cifukwa cace atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zopunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzace adzatayika.

22 Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu ucokera kumpoto; ndi mtundu waukuru adzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.

23 Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.

24 Tamva ife mbiri yace; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.

25 Usaturukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.

26 Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udzibveke ndi ciguduli, ndi kubvimbvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.

27 Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.

28 Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi citsulo; onsewa acita mobvunda;

29 mbvukuto yatenthedwa ndi moto; mthobvu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga cabe; pakuti oipa sacotsedwa.

30 Anthu adzawacha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo.