1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti,
2 Pita ku nyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m'nyumba ya Yehova, m'cipinda cina, nuwapatse iwo vinyo amwe.
3 Ndipo ndinatenga Yaasaniya mwana wa Yeremiya, mwana wa Habazinya, ndi abale ace, ndi ana amuna ace, ndi nyumba yonse ya Arekabu;
4 ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'cipinda ca ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, cokhala pambali pa cipinda ca akuru, ndico cosanjika pa cipinda ca Maseya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;
5 ndipo ndinaika pamaso pa ana amuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo.
6 Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kumuyaya;
7 ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo.
8 Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m'zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu amuna ndi akazi;
9 ngakhale kudzimangira nyumba zokhalamo; ndipo sitiri nao munda wamphesa, kapena munda, kapena mbeu;
10 koma takhala m'mahema, ntimvera, nticita monga mwa zonse anatiuza Yonadabu kholo lathu.
11 Koma panali, pamene Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu cifukwa tiopa nkhondo ya Akasidi, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala m'Yerusalemu.
12 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,
13 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala m'Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga ati Yehova.
14 Mau a Yonadabu mwana wa Rekabu, amene anauza ana ace, asamwe vinyo, alikucitidwa, ndipo mpaka lero samamwa, pakuti amvera lamulo la kholo lao; koma Ine ndanena ndi inu, ndalawirira ndi kunena; koma simunandimvera Ine.
15 Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yace yoipa, konzani macitidwe anu, musatsate milungu yina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunandichera khutu lanu, simunandimvera Ine.
16 Pakuti monga ana a Yonadabu mwana wa Rekabu acita lamulo la kholo lao limene anawauza, koma anthu awa sanandimvera Ine.
17 Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala m'Yerusalemu coipa conseco ndawanenera iwo; cifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandibvomera.
18 Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Cifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kucita monga mwa zonse anakuuzani inu;
19 cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wakuima pamaso panga kumuyaya.