1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m'maunyolo pamodzi ndi am'nsinga onse a Yerusalemu ndi Yuda, amene anatengedwa am'nsinga kunka nao ku Babulo.
2 Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera coipa ici malo ano;
3 ndipo Yehova wacitengera, ndi kucita monga ananena, cifukwa mwacimwira Yehova, ndi kusamvera mau ace, cifukwa cace cinthu ici cakufikirani.
4 Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babulo, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babulo, tsala; taona, dziko lonse liri pamaso pako; kuli konse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.
5 Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babulo inamyesa wolamulira midzi ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kuli konse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke.
6 Ndipo Yeremiya ananka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa, nakhala kumeneko kwa anthu otsala m'dziko.
7 Ndipo pamene akuru onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babulo adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwa ndende kunka nao ku Babulo;
8 pamenepo anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, ndi Saraya mwana wa Tanumeti, ndi ana a Efai wa ku Netofa, ndi Jezaniya mwana wa munthu wa ku Maaka, iwo ndi anthu ao.
9 Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Akasidi; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babulo, ndipo kudzakukomerani.
10 Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Akasidi, amene adzadza kwa ife; koma inu, sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda.
11 Comweco pamene Ayuda onse okhala m'Moabu ndi mwa ana a Amoni, ndi m'Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babulo inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;
12 pamenepo Ayuda onse anabwerera kufumira ku malo onse kumene anawaingitsirako, nafika ku dziko la Yuda, kwa Gedaliya, ku Mizipa, nasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamalimwe zambiri.
13 Ndiponso Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala m'minda, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa,
14 nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismayeli mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvera iwo.
15 Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismayeli mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; cifukwa canji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?
16 Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anati kwa Yohanani mwana wa Kareya, Usacite ici; pakuti unamizira Ismayeli.