Yeremiya 41 BL92

Gedaliya ndi ena aphedwa ndi Ismayeli

1 Ndipo panali mwezi wacisanu ndi ciwiri, Ismayeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkuru wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi m'Mizipa.

2 Ndipo anauka Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babulo inamuika wolamulira dziko.

3 Ismayeli naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Akasidi amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo.

4 Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,

5 anadza anthu ocokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndebvu zao, atang'amba zobvala zao, atadzitematema, ana tenga nsembe zaufa ndi zonunkhira m'manja mwao, kunka nazo ku nyumba ya Yehova.

6 Ndipo Ismayeli mwana wa Netaniya anaturuka m'Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wace wa Ahikamu.

7 Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mudzi, Ismayeli mwana, wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.

8 Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismayeli, Musatiphe ife; pakuti tiri ndi cuma cobisika m'mudzi, ca tirigu, ndi ca barele, ndi ca mafuta, ndi ca uci. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.

9 Ndipo dzenje moponyamo Ismayeli mitembo yonse ya anthu amene anawapha, cifukwa ca Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa cifukwa ca kuopa Raasa mfumu ya Israyeli, lomwelo Ismayeli mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.

10 Ndipo Ismayeli anatenga ndende otsala onse a anthu okhala m'Mizipa, ana akazi a mfumu, ndi-anthu onse amene anatsala m'Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismayeli mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.

11 Koma pamene Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe Onse a nkhondo akhala naye, anamva zoipa zonse anazicita Ismayeli mwana wa Netaniya,

12 anatenga anthu onse, nanka kukamenyana ndi Ismayeli mwana wa Netaniya, nampeza pa madzi ambiri a m'Gibeoni.

13 Ndipo panali pamene anthu onse amene anali ndi Ismayeli anaona Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, anasekera.

14 Ndipo anthu onse amene Ismayeli anatenga ndende kuwacotsa m'Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wace wa Kareya,

15 Koma Ismayeli mwana wace wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni.

16 Ndipo Yohanani mwana wace wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismayeli mwana wace wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibeoni;

17 ndipo anacoka, natsotsa m'Geruti-Kimamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa m'Aigupto,

18 cifukwa ca Akasidi; pakuti anawaopa, cifukwa Ismayeli mwana wace wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wace wa Akikamu, amene mfumu ya ku Babulo anamuika wolamulira m'dzikomo.