1 Mau amene ananena Yehova za Babulo, za dziko la Akasidi, mwa Yeremiya mneneri.
2 Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babulo wagwidwa, Beli wacitidwa manyazi, Merodake watyokatyoka, zosema zace zacitidwa manyazi, mafano ace atyokatyoka.
3 Pakuti mtundu wa anthu udzaturuka kumpoto kudzamenyana naye, udzacititsa dziko lace bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama.
4 Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, ana a Israyeliadzadza, iwo ndi ana a Yuda; pamodzi adzayenda m'njira mwao alinkulira, nadzafuna Yehova Mulungu wao.
5 Adzafunsira Ziyoni nkhope zao zirikuyang'ana kumeneko, ndi kuti, Tiyeni inu, dzilumikizeni kwa Yehova m'cipangano ca muyaya cimene sicidzaiwalika.
6 Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; acoka kuphiri kunka kucitunda; aiwala malo ao akupuma.
7 Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitiparamula mlandu, cifukwa iwo anacimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, ciyembekezo ca atate ao.
8 Thawani pakati pa Babulo, turukani m'dziko la Akasidi, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta.
9 Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babulo msonkhano wa mitundu yaikuru kucokera ku dziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babulo adzacotsedwa; mibvi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera cabe.
10 Ndipo Kasidi adzakhala cofunkha; onse amene amfunkhitsa iye adzakhuta, ati Yehova.
11 Cifukwa mukondwa, cifukwa musekerera, inu amene mulanda colowa canga, cifukwa muli onenepa monga ng'ombe yamsoti yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;
12 amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, cipululu, dziko louma, bwinja.
13 Cifukwa ca mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babulo adzadabwa, adzatsonyera pa zobvuta zace zonse.
14 Gubani ndi kuzungulira Babulo kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mibvi; pakuti wacimwira Yehova.
15 Mumpfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ace agwa; makoma ace agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; mumbwezere cilango; monga iye wacita mumcitire iye momwemo.
16 Muwathe ofesa ku Babulo, ndi iwo amene agwira zenga nyengo ya masika; cifukwa ca lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ace, nadzathawira yense ku dziko lace.
17 Israyeli ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampitikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asuri; ndipo pomariza Nebukadirezara uyo watyola mafupa ace.
18 Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzalanga mfumu ya ku Babulo ndi dziko lace, monga ndinalanga mfumu ya Asuri.
19 Ndipo ndidzabwezeranso Israyeli ku busa lace, ndipo adzadya pa Karimeli ndi pa Basana, moyo wace nudzakhuta pa mapiri a Efraimu ndi m'Gileadi.
20 Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israyeli zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zocimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati cotsala.
21 Kwera kukamenyana ndi dziko la Merataimu, ndi okhala m'Pekoli, ipha nuononge konse pambuyo pao, ati Yehova, cita monga mwa zonse ndinakuuza iwe.
22 Phokoso la nkhondo liri m'dziko lino, ndi lakuononga kwakukuru.
23 Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kutyoka! Babulo wasandulca bwinja pakati pa amitundu!
24 Ndakuchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babulo, ndipo sunadziwa, wapezeka, ndiponso wagwidwa, cifukwa walimbana ndi Yehova.
25 Yehova watsegula pa nyumba ya zida zace, ndipo waturutsa zida za mkwiyo wace; pakuti Ambuye Yehova wa makamu, ali ndi nchito m'dziko la Akasidi.
26 Tadzani kudzamenyana ndi iye kucokera ku malekezero ace, tsegulani pa nkhokwe zace; unjikani zace monga miyulu, mumuononge konse; pasatsale kanthu ka pa iye.
27 Iphani ng'ombe zamphongo zace zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.
28 Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babulo, kuti alalikire m'Ziyoni kubwezera cilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.
29 Memezani amauta amenyane ndi Babulo, onse amene akoka uta; mummangire iye zitando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wace yense; mumbwezere iye monga mwa nchito yace; monga mwa zonse wazicita, mumcitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israyeli.
30 Cifukwa cace anyamata ace adzagwa m'miseu yace, ndi anthu ankhondo ace onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova.
31 Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.
32 Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'midzi yace, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.
33 Yehova wa makamu atero: Ana a Israyeli ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.
34 Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lace Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumitse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babulo.
35 Lupanga liri pa Akasidi, ati Yehova, pa okhala m'Babulo, pa akuru ace, ndi pa anzeru ace.
36 Lupanga liri pa amatukutuku, ndipo adzapusa; lupanga liri pa anthu olimba ace, ndipo adzaopa.
37 Lupanga liri pa akavalo ao, ndi pa magareta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pace, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga liri pa cuma cace, ndipo cidzalandidwa.
38 Cirala ciri pa madzi ace, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaruka ndi kufuna zoopsa.
39 Cifukwa cace zirombo za kucipululu ndi mimbulu zidzakhalamo, ndi nthiwatiwa zidzakhala m'menemo; ndipo sadzakhalamo anthu konse; ndipo sadzakhalamo m'mibadwo mibadwo.
40 Monga muja Yehova anagwetsa Sodomu ndi Gomora ndi midzi Inzace, ati Yehova; anthu sadzakhalamo, mwana wa munthu sadzagonamo.
41 Taonani, anthu acokera kumpoto; ndiwo mtundu waukuru, ndipo mafumu ambiri adzaukitsidwa kucokera ku malekezero a dziko lapansi.
42 Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babulo.
43 Mfumu ya ku Babulo yamva mbiri yao, ndipo manja ace alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala.
44 Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wocokera ku Yordano wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umcokere, ndipo ali yense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wace; pakuti wakunga Ine ndani? adzandiikira nthawi ndani? ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?
45 Cifukwa cace tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babulo; ndi zimene walingirira dziko la Akasidi; ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.
46 Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babulo, ndipo mpfuu wamveka mwa amitundu.