Yeremiya 14 BL92

Yeremiya apempherera anthu

1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za cirala.

2 Yuda alira, ndipo zipata zace zilefuka, zikhala pansi zobvekedwa ndi zakuda; mpfuu wa Yerusalemu wakwera.

3 Akuru ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, apfunda mitu yao.

4 Cifukwa ca nthaka yocita ming'aru, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, apfunda mitu yao.

5 Inde, nswalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ace, cifukwa mulibe maudzu.

6 Mbidzi zinaima pamapiri oti se, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, cifukwa palibe maudzu.

7 Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, citani Inu cifukwa ca dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zacuruka; takucimwirani Inu.

8 Inu, ciyembekezo ca Israyeli, mpulumutsi wace nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?

9 Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, tichedwa ndi dzina lanu; musatisiye.

Yehova osamvera pempherolo

10 Atero Yehova kwa anthu awa, Comwecoakonda kusocerera; sanakaniza mapazi ao; cifukwa cace. Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira coipa cao, nadzalanga zocimwa zao.

11 Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.

12 Pamene asala cakudya, sindidzamva kupfuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi cirala, ndi caola.

13 Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi cirala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.

14 Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi cinthu cacabe, ndi cinyengo ca mtima wao.

15 Cifukwa cace atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatuma, koma ati, Lupanga ndi cirala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi cirala aneneriwo adzathedwa.

16 Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu cifukwa ca cirala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna ndi akazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.

17 Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukuru, ndi bala lopweteka kwambiri.

18 Ndikaturukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.

19 Kodi mwakanadi Yuda? kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? bwanji mwatipanda ife, ndipo tiribe kucira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakucira, ndipo taonani mantha!

20 Tibvomereza, Yehova, cisalungamo cathu, ndi coipa ca makolo athu; pakuti takucimwirani Inu.

21 Musatinyoze ife, cifukwa ca dzina lanu; musanyazitse mpando wacifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.

22 Mwa zacabe za mitundu ya anthu ziripo kodi, zimene zingathe kubvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.