Yeremiya 51 BL92

1 Yehova atero: Taonani, ndidzaukitsira Babulo, ndi iwo okhala m'Lebi-kamai, mphepo yoononga,

2 Ndipo ndidzatuma ku Babulo alendo, amene adzamkupira iye, amene adzataya zonse m'dziko lace, pakuti tsiku la cisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pace.

3 Wauta asakoke uta wace, asadzikweze m'malaya ace acitsulo; musasiye anyamata ace; muononge ndithu khamu lace lonse.

4 Ndipo adzagwa ophedwa m'dziko la Akasidi, opyozedwa m'miseu yace.

5 Pakuti Israyeli ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi ucimo kucimwira Woyera wa Israyeli.

6 Thawani pakati pa Babulo, yense apulumuke moyo wace; musathedwe m'coipa cace; pakuti ndi nthawi ya kubwezera cilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yace.

7 Babulo wakhala cikho cagolidi m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wace; cifukwa cace amitundu ali ndi misala.

8 Babulo wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zace bvunguti, kapena angacire.

9 Tikadaciritsa Babulo koma sanacire; mumsiye iye, tipite tonse yense ku dziko lace; pakuti ciweruziro cace cifikira kumwamba, cinyamulidwa mpaka kuthambo,

10 Yehova waturutsa cilungamo cathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni nchito ya Yehova Mulungu wathu.

11 Nolani mibvi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; cifukwa alingalirira Babulo kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.

12 Muwakwezere mbendera makoma a Babulo, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kucita comwe ananena za okhala m'Babulo.

13 Iwe wokhala pa madzi ambiri, wocuruka cuma, cimariziro cako cafika, cilekezero ca kusirira kwako.

14 Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mpfuu.

15 Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yace, ndi luso anayala thambo;

16 pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, aturutsa mphepo ya m'nyumba za cuma zace.

17 Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golidi acitidwa manyazi ndi fanizo lace losema; pakuti fanizo lace loyenga liri bodza, mulibe mpweya m'menemo.

18 Ngwacabe, ciphamaso; nthawi yakulangidwa kwao adzatayika.

19 Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndi mtundu wa colowa cace, dzina lace ndi Yehova wa makamu.

20 Iwe ndiwe cibonga canga ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzatyolatyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu;

21 ndi iwe ndidzatyolatyola kavalo ndi wakwera wace;

22 ndi iwe ndidzatyolatyola gareta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzatyolatyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzatyolatyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzatyolatyola mnyamata ndi namwali;

23 ndi iwe ndidzatyolatyola mbusa ndi zoweta zace; ndi iwe ndidzatyolatyola wakulima ndi gori la ng'ombe lace; ndi iwe ndidzatyolatyola akazembe ndi ziwanga,

24 Ndipo ndidzabwezera Babulo ndi okhala m'Kasidi zoipa zao zonse anazicita m'Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.

25 Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa.

26 Ndipo sadzacotsa pa iwe mwala wa pangondya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova.

27 Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenaza; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati mandowa.

28 Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ace, ndi ziwanga zace zonse, ndi dziko lonse la ufumu wace.

29 Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babulo ziripobe, zoti ayese dziko la Babulo bwinja lopanda wokhalamo.

30 Olimba a ku Babulo akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zace zapsya ndi moto; akapici ace atyoka.

31 Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzace, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzace, kukauza mfumu ya ku Babulo kuti mudzi wace wagwidwa ponsepo;

32 pamadooko patsekedwa, pamatamanda a mabango patenthedwa ndi moto, ndi anthu a nkhondo aopa.

33 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Mwana wamkazi wa Babulo akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang'ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye.

34 Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwace ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine,

35 Wokhala m'Ziyoni adzati, Ciwawa anandicitira ine ndi thupi langa cikhale pa Babulo; nadzati Yerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala m'Kasidi.

36 Cifukwa cace Yehova atero: Taona, ndidzanenera iwe mlandu wako, ndidzawabwezera cilango cifukwa ca iwe; ndidzaphwetsa nyanja yace, ndidzaphwetsa citsime cace.

37 Ndipo Babulo adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, cizizwitso, cotsonyetsa, wopanda okhalamo.

38 Adzabangula pamodzi ngati misona ya mikango; adzacita nthulu ngati ana a mikango.

39 Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone cigonere, asanyamuke, ati Yehova.

40 Ndidzawagwetsa kuti aphedwe manga nkhosa zamphongo, ndi atonde.

41 Sesake wagwidwatul cimene dziko lonse lapansi linacitamanda calandidwa dzidzidzi Babulo wakhalatu bwinja pakati pa amitundu

42 Nyanja yakwera kufikira ku Babulo; wamira ndi mafunde ace aunyinji.

43 Midzi yace yakhala bwinja, dziko louma, cipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu ali yense.

44 Ndipo Ine ndiweruza Beli m'Babulo, ndipo ndidzaturutsa m'kamwa mwace comwe wacimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babulo lidzagwa.

45 Anthu anga, turukani pakati pace, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo waukali wa Yehova.

46 Mtima wanu usalefuke, musaope cifukwa ca mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika caka cina, pambuyo pace caka cina mbiri yina, ndi ciwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.

47 Cifukwa cace, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babulo, ndipo dziko lace lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ace onse adzagwa pakati pace.

48 Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse ziri m'menemo, zidzayimba mokondwerera Babulo; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kucokera kumpoto, ati Yehova.

49 Monga Babulo wagwetsa ophedwa a Israyeli, momwemo pa Babulo padzagwa ophedwa a dziko lonse.

50 Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu, musaime ciimire; mukumbukire Yehova kutari, Yerusalemu alowe m'mtima mwanu.

51 Tiri ndi manyazi, cifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m'malo opatulika a nyumba ya Yehova.

52 Cifukwa cace, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ace; ndipo pa dziko lace lonse olasidwa adzabuula.

53 Ngakhale Babulo adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yace, koma kucokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.

54 Mau akupfuula ocokera ku Babulo, ndi a cionongeko cacikuru ku dziko la Akasidi!

55 pakuti Yehova afunkha Babulo, aononga m'menemo mau akuru; ndipo mafunde ace adzakokoma ngati madzi ambiri, mau ao aphokosera;

56 pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babulo, ndi anthu ace olimba agwidwa, mauta ao atyokatyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu.

57 Ndipo ndidzaledzeretsa akuru ace ndi anzeru ace, akazembe ace ndi ziwanga zace, ndi anthu ace olimba; ndipo adzagona cigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lace ndi Yehova wa makamu.

58 Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babulo adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zace zazitari zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira nchito cabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.

59 Mau amene Yeremiya mneneri anauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babulo caka cacinai ca ufumu wace. Ndipo Seraya anali kapitao wa cigono cace.

60 Ndipo Yeremiya analemba m'buku coipa conse cimene cidzafika pa Babulo, mau onse awa olembedwa za Babulo.

61 Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babulo, samalira kuti uwerenge mau awa onse,

62 nuti, inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi.

63 Ndipo padzakhala, utatha kuwerenga buku ili, Ib ulimange ndi mwala, nuliponye pakati pa Firate;

64 nuti, Comweco adzamira Babulo, sadzaukanso cifukwa ca coipa cimene ndidzamtengera iye; ndipo adzatopa.Mau a Yeremiya ndi omwewo.