1 Ndipo panali caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,
2 Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israyeli, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse, kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.
3 Kapena nyumba ya Yuda idzamva coipa conse cimene nditi ndidzawacitire; kuti abwerere yense kuleka njira yace yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi cimo lao.
4 Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m'buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.
5 Ndipo Yeremiya anauza Baruki, kuti, Ndaletsedwa sindithai kulowa m'nyumba ya Yehova;
6 koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene aturuka m'midzi yao.
7 Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yace yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukuru.
8 Ndipo Baruki mwana wa Neriya anacita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri, nawerenga m'buku mau a Yehova m'nyumba ya Yehova.
9 Ndipo panali caka cacisanu ca Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wacisanu ndi cinai, anthu onse a m'Yerusalemu, ndi anthu onse ocokera m'midziya Yuda kudzaku Yerusalemu, analalikira kusala kudya pamaso pa Yehova.
10 Ndipo Baruki anawerenga m'buku mau a Yeremiya m'nyumba ya Yehova, m'cipinda ca Gemariya mwana wa Safani mlembi, m'bwalo la kumtunda, pa khomo la cipata catsopano ca nyumba ya Yehova, m'makutu a anthu onse.
11 Pamene Mikaya mwana wa Hemariya, mwana wa Safani, anamva m'buku mau onse a Yehova,
12 anatsikira ku nyumba ya mfumu, nalowa m'cipinda ca mlembi; ndipo, taonani, akuru onse analikukhalamo, Elisama mlembi, ndi Delaya mwana wa Semaya, ndi Elinatani mwana wa Akibori, ndi Gemariya mwana wa Safani, ndi Zedekiya mwana wa Hananiya, ndi akuru onse.
13 Ndipo Makaya anafotokozera iwo mau onse amene anamva, pamene Baruki anawerenga buku m'makutu a anthu.
14 Cifukwa cace akuru onse anatuma Yehudi mwana wa Nataniya, mwana wa Salamiya, mwana wa Kusa, kwa Baruki, kukanena, Tenga m'dzanja lako mpukutu wauwerenga m'makutu a anthu, nudze kuno. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo m'dzanja lace, nadza kwa iwo.
15 Ndipo anati kwa iye, Khala pansi tsopano, nuwerenge m'makutu athu. Ndipo Baruki anauwerenga m'makutu ao.
16 Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzace, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.
17 Ndipo anamfunsa Baruki, kuti, Utifotokozeretu, Unalemba bwanji mau awa onse ponena iye?
18 Ndipo Baruki anayankha iwo, Pakamwa pace anandichulira ine mau awa onse, ndipo ndinawalemba ndi inki m'bukumo.
19 Ndipo akuru anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli.
20 Ndipo analowa kwa mfumu kubwalo; ndipo anasunga buku m'cipinda ca Elisama mlembi; nafotokozera mau onse m'makutu a mfumu.
21 Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kuturuka nao m'cipinda ca Elisama mlembi, Ndipo Yehudi anauwerenga m'makutu a mfumu, ndi m'makutu a akuru onse amene anaima pambali pa mfumu.
22 Ndipo mfumu anakhala m'nyumba ya nyengo yacisanu mwezi wacisanu ndi cinai; ndipo munali moto m'nkhumbaliro pamaso pace.
23 Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m'moto wa m'nkhumbaliromo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m'nkhumbaliromo.
24 Ndipo sanaopa, sanang'ambe nsaru zao, kapena mfumu, kapena atumiki ace ali yense amene anamva mau onsewa.
25 Tsononso Elinatani ndi Deliya ndi Gemariya anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera.
26 Ndipo mfumu inauza Yeremeeli mwana wace wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Azirieli, ndi Selemiya mwana wa Abidieli, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.
27 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, mfumu itatentha mpukutuwo, ndi mau amene analemba Baruki ponena Yeremiya, kuti,
28 Tenganso mpukutu wina, nulembe m'menemo mau oyamba aja anali mu mpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wautentha.
29 Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m'menemo, kuti, Mfumu ya ku Babulo idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m'menemo anthu ndi nvama?
30 Cifukwa cace Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wacifumu wa Davide; ndipo mtembo wace udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli cisanu.
31 Ndipo ndidzamlanga iye ndi mbeu zace ndi atumiki ace cifukwa ca mphulupulu zao; ndipo ndidzawatengera iwo, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, zoipa zonse ndawanenera iwo, koma sanamvera.
32 Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.