Yesaya 56 BL92

Malonjezo a kwa iwo osunga Sabata

1 Atero Yehova, Sungani inu ciweruziro, ndi kucita cilungamo; pakuti cipulumutso canga ciri pafupi kudza, ndi cilungamo canga ciri pafupi kuti cib zumbulutsidwe,

2 Wodala munthu amene acita ici, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ici, amene asunga sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lace osacita nalo coipa ciri conse.

3 Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ace; pena mfule asanene, Taonani ine ndiri mtengo wouma.

4 Pakuti atero Yehova kwa mifule imene isunga masabata, nisankha zinthu zimene zindikondweretsa Ine, nigwira zolimba cipangano canga,

5 Kwa iyo ndidzapatsa m'nyumba yanga ndi m'kati mwa makoma anga malo, ndi dzina loposa la ana amuna ndi akazi; ndidzawapatsa dzina lacikhalire limene silidzadulidwa.

6 Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ace, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba cipangano canga;

7 naonso ndidzanka nao ku phiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa pa guwa la nsembe langa; pakuti nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.

8 Ambuye Yehova amene asonkhanitsa otayika a Israyeli ati, Komabe ndidzasonkhanitsa ena kwa iye, pamodzi ndi osonkhanitsidwa ace ace.

9 Inu zirombo zonse za m'thengo, idzani kulusa, inde zirombo inu nonse za m'nkhalango.

10 Alonda ace ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agaru acete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.

11 Inde agaru ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira ku njira zao, yense kutsata phindu lace m'dera lace.

12 Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta cakumwa caukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikuru loposa ndithu.