Yesaya 14 BL92

1 Pakuti Ambuye adzamcitira cifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israyeli, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo acilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza ku nyumba ya Yakobo.

2 Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa ku malo a kwao; ndipo a nyumba ya Israyeli adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisrayeli adzalamulira owabvuta.

3 Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa cisoni cako, ndi nsautso yako, ndi nchito yako yobvuta, imene anakugwiritsa,

4 pamenepo udzayimbira mfumu ya ku Babulo nyimbo iyi yancinci, ndi kuti, Wobvuta wathadi! mudzi wagolidi wathadi!

5 Yehova watyola mkunkhu wa woipa, ndodo yacifumu ya wolamulira.

6 Wokantha anthu mwaukali kuwakantha cikanthire, wolamulira amitundu mokwiya, angosautsidwa wopanda womlanditsa.

7 Dziko lonse lapuma, liri du; iwo ayamba kuyimba nyimbo,

8 Inde, milombwa ikondwera ndi iwe, ndi mikungudza ya Lebano, ndi kunena, Cigwetsere iwe pansi, palibe wokwera kudzatidula ife.

9 Kunsi kwa manda kugwedezeka, cifukwa ca iwe, kukucingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuru akuru a dziko lapansi; kukweza kucokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.

10 Onse adzabvomera, nadzati kwa iwe, Kodi iwe wakhalanso wopanda mphamvu ngati ife? kodi iwe wafanana nafe?

11 Cifumu cako catsitsidwa kunsi ku manda, ndi phokoso la mingoli yako; mbozi zayalidwa pansi pa iwe, ndi mphukutu zakukuta.

12 Wagwadi kucokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbanda kuca! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!

13 Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wacifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;

14 ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.

15 Koma udzatsitsidwa kunsi ku manda, ku malekezero a dzenje.

16 Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;

17 amene anapululutsa dziko, napasula midzi yace, amene sanamasula ndende zace, zinke kwao?

18 Mafumu onse a amitundu, onsewo agona m'ulemerero yense kunyumba kwace.

19 Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati cobvala ca ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira ku miyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.

20 Iwe sudzaphatikizidwa pamodzi nao poikidwa, pakuti iwe waononga dziko lako, wapha anthu ako; mbeu ya ocita zoipa sidzachulidwa konse.

21 Konzani inu popherapo ana ace, cifukwa ca kuipa kwa atate ao; kuti iwo asadzauka ndi kukhala nalo dziko, ndi kudzaza dziko lapansi ndi midzi.

22 Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babulo dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi cidzukulu cacimuna, ati Yehova.

23 Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi madziwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsace la cionongeko, ati Yehova wa makamu.

Aneneratu za kutyoka kwa Asuri

24 Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, cotero cidzacitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, cotero cidzakhala;

25 kuti Ine ndidzatyola Asuri m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo gori lace lidzacoka pa iwo, ndi katundu wace adzacoka paphuzi pao.

26 Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.

27 Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? ndi dzanja lace latambasulidwa, ndani adzalibweza?

Aneneratu za tsoka la Afilisti

28 Caka cimene mfumu Ahazi anamwalira katundu amene analipo.

29 Usakondwere, lwe Filistia, wonsewe, potyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzaturuka mphiri, ndimo cipatso cace cidzakhala njoka yamoto youluka.

30 Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa.

31 Lira, cipata iwe; pfuula, mudzi iwe; wasungunuka, Filistia wonsewe, pakuti utsi ucokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yace.

32 Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ace obvutidwa adzaona pobisalira.