1 Bwenzi lako wapita kuti,Mkaziwe woposa kukongola?Bwenzi lako wapambukira kuti,Tikamfunefune pamodzi nawe?
2 Bwenzi langa watsikira kumunda kwace,Ku zitipula za mphoka, Kukadya kumunda kwace, ndi kuchera akakombo.
3 Ndine wace wa wokondedwa wanga, wokondedwa wanganso ndiye wa ine;Aweta zace pakati pa akakombo.
4 Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza,Wokoma ngati Yerusalemu,Woopsya ngati nkhondo ndi mbendera.
5 Undipambutsire maso ako, Pakuti andiopetsa.Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,Zigona pambali pa Gileadi.
6 Mano ako akunga gulu la nkhosa zazikazi,Zikwera kucokera kosamba; Yonse iri ndi ana awiri,Palibe imodzi yopoloza.
7 Palitsipa pako pakunga phande la khangazaPatseri pa cophimba cako.
8 Alipo akazi akulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi,Kudza akazi ang'ono makumi asanu ndi atatu,Ndi anamwali osawerengeka.
9 Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi;Ndiye wobadwa yekha wa amace;Ndiye wosankhika wa wombala.Ana akazi anamuona, namucha wodala;Ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi ang'ono namtamanda.
10 Nati, Ndaniyo aturuka ngati mbanda kuca,Wokongola ngati mwezi,Woyera ngati dzuwa,Woopsya ngati nkhondo ndi mbendera?
11 Ndinatsikira ku munda wa ntedza,Kukapenya msipu wa m'cigwa,Kukapenya ngati pamipesa paphuka,Ngati pamakangaza patuwa maluwa.
12 Ndisanazindikire, moyo wanga unandiimikaPakati pa magareta a anthu anga aufulu.
13 Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe;Bwera, bwera, tiyang'ane pa iwe.Muyang'aniranji pa Msulami,Ngati pa masewero akuguba?