Nyimbo 4 BL92

Mkwati alemekeza mkwatibwi

1 Taona, wakongola, bwenzi langa, namwaliwe, taona, wakongola;Maso ako akunga a nkhunda patseri pa cophimba cako:Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,Zooneka pa phiri la Gileadi.

2 Mano ako akunga gulu la nkhosa zosengasenga,Zokwera kucokera kosamba;Yonse iri ndi ana awiri,Palibe imodzi yopoloza.

3 Milomo yako ikunga mbota yofiira,M'kamwa mwako ndi kukoma:Palitsipa pako pakunga phande la khangazaPatseri pa cophimba cako.

4 Khosi lako likunga nsanja ya Davide anaimangira zida,Apacikapo zikopa zikwi,Ngakhale zikopa zonse za amuna amphamvu,

5 Maere ako awiri akunga ana awiri a nswala obadwa limodzi,Akudya pakati pa akakombo.

6 Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,Ndikamuka ku phiri la nipa,Ndi ku citunda ca mtanthanyerere.

7 Wakongola monse monse, wokondedwa wanga, namwaliwe,Mulibe cirema mwa iwe.

8 Idza nane kucokera ku Lebano, mkwatibwi,Kucokera nane ku Lebano:Unguza pamwamba pa Amana,Pa nsonga ya Seniri ndi Hermoni,Pa ngaka za mikango,Pa mapiri a anyalugwe.

9 Walanda mtima wanga, mlongwanga, mkwatibwi;Walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi,Ndi cinganga cimodzi ca pakhosi pako,

10 Ha, cikondi cako ncokongola, mlongwanga, mkwatibwi!Kodi cikondi cako siciposa vinyo?Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundu mitundu!

11 M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uci,Uci ndi mkaka ziri pansi pa lilime lako;Kununkhira kwa zobvala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebano,

12 Mlongwanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa;Ngati kasupe wotsekedwa, ndi citsime copikiza.

13 Mphukira zako ndi munda wamakangaza,Ndi zipatso zofunika, bonongwe ndi mphoka,

14 Mphoka ndi cikasu,Nzimbe ndi ngaho, ndi mitengo yonse yamtanthanyerere;Nipa ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka.

15 Ndiwe kasupe wa m'minda,Citsime ca madzi amoyo,Ndi mitsinje yoyenda yocokera ku Lebano.

Ayankha mkwatibwi

16 Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kumwela;Nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zace ziturukemo.Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwace,Nadye zipatso zace zofunika.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8