3 Alonda akuyendayenda m'mudzi anandipeza:Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?
4 Nditawapitirira pang'ono,Ndinampeza amene moyo wanca umkonda:Ndinamgwiriziza, osamfumbatula,Mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai,Ngakhale m'cipinda ca wondibala.
5 Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Pali mphoyo, ndi nswala ya kuthengo,Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi,Mpaka cikafuna mwini.
6 Ndaniyu akwera kuturuka m'cipululu ngati utsi wa tolo,Wonunkhira ndi nipa ndi mtanthanyerere,Ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?
7 Taonani, ndi macila a Solomo;Pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi,A mwa ngwazi za Israyeli.
8 Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:Yense ali ndi lupanga lace pancafu pace,Cifukwa ca upandu wa usiku.
9 Solomo mfumu anadzipangira macila okhalamo tsongaNdi matabwa a ku Lebano.