3 Ndine wace wa wokondedwa wanga, wokondedwa wanganso ndiye wa ine;Aweta zace pakati pa akakombo.
4 Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza,Wokoma ngati Yerusalemu,Woopsya ngati nkhondo ndi mbendera.
5 Undipambutsire maso ako, Pakuti andiopetsa.Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,Zigona pambali pa Gileadi.
6 Mano ako akunga gulu la nkhosa zazikazi,Zikwera kucokera kosamba; Yonse iri ndi ana awiri,Palibe imodzi yopoloza.
7 Palitsipa pako pakunga phande la khangazaPatseri pa cophimba cako.
8 Alipo akazi akulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi,Kudza akazi ang'ono makumi asanu ndi atatu,Ndi anamwali osawerengeka.
9 Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi;Ndiye wobadwa yekha wa amace;Ndiye wosankhika wa wombala.Ana akazi anamuona, namucha wodala;Ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi ang'ono namtamanda.