2 Pamcombo pako pakunga cikho coulungika,Cosasowamo vinyo wosanganika:Pamimba pako pakunga mulu wa tiriguWozingidwa ndi akakombo.
3 Maere ako akunga ana awiri a nswalaAnabadwa limodzi.
4 Khosi lako likunga nsanja yaminyanga;Maso ako akunga matawale a ku Hesiboni,A pa cipata ca Batirabimu;Mphuno yako ikunga nsanja ya ku LebanoImene iloza ku Damasiko.
5 Mutu wako ukunga Karimeli,Ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsaru yakuda;Mfumu yamangidwa ndi nkhata zace ngati wamsinga.
6 Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika,Bwenziwe, m'zokondweretsa!
7 Msinkhu wakowu ukunga mlaza,Maere ako akunga matsango amphesa,
8 Ndinati, Ndikakwera pamlazapo,Ndikagwira nthambi zace:Maere ako ange ngati matsango amphesa,Ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula;