7 Msinkhu wakowu ukunga mlaza,Maere ako akunga matsango amphesa,
8 Ndinati, Ndikakwera pamlazapo,Ndikagwira nthambi zace:Maere ako ange ngati matsango amphesa,Ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula;
9 M'kamwa mwako munge ngati vinyo woposa,Womeza tseketeke bwenzi langa,Wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.
10 Ndine wa wokondedwa wanga mnyamatayo,Ndine amene andifunayo.
11 Tiye, bwenzi langa, tinke kuminda;Titsotse m'miraga.
12 Tilawire kunka ku minda yamipesa;Tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso,Makangaza ndi kutuwa maluwa ace;Pompo ndidzakupatsa cikondi canga,
13 Mandimu anunkhira,Ndi pamakomo pathu zipatso zabwino, za mitundu mitundu, zakale ndi zatsopano,Zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga.