3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosabvomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi ciphunzitsoco ciri monga mwa cipembedzo:
4 iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayarukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zieokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;
5 makani opanda pace a anthu oipsika nzeru ndi ocotseka coonadi, akuyesa kuti cipembedzo cipindulitsa.
6 Koma cipembedzo pamodzi ndi kudekha cipindulitsa kwakukuru;
7 pakuti sitinatenga kanthu polowa m'dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pocoka pano;
8 koma pokhala nazo zakudya ndizopfunda, zimenezi zitikwanire.
9 Koma iwo akufuna kukhala acuma amagwa m'ciyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'cionongekondi citayiko.