8 koma pokhala nazo zakudya ndizopfunda, zimenezi zitikwanire.
9 Koma iwo akufuna kukhala acuma amagwa m'ciyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'cionongekondi citayiko.
10 Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo cikondi ca pa ndalama; cimene ena pocikhumba, anasocera, nataya cikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.
11 Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate cilungamo, cipembedzo, cikhulupiriro, cikondi, cipiriro, cifatso.
12 Limba nayo nkhondo yabwino ya cikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wabvomereza cibvomerezo cabwino pamaso pa mboni zambiri.
13 Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Kristu Yesu, amene anacitira umboni cibvomerezo cabwino kwa Pontiyo Pilato;
14 kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda cirema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu;