2 Cisomo kwa inu, ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.
3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Kristu;
4 monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi,
5 Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana, a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace,
6 kuti uyamikidwe ulemerero wa cisomo cace, cimene anaticitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.
7 Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wace, cikhululukiro ca zocimwa, monga mwa kulemera kwa cisomo cace,
8 cimene anaticurukitsira ife m'nzeru zonse, ndi cisamaliro.