6 kuti uyamikidwe ulemerero wa cisomo cace, cimene anaticitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.
7 Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wace, cikhululukiro ca zocimwa, monga mwa kulemera kwa cisomo cace,
8 cimene anaticurukitsira ife m'nzeru zonse, ndi cisamaliro.
9 Anatizindikiritsa ife cinsinsi ca cifuniro cace, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa iye,
10 kuti pa tnakonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.
11 Mwa iye tinayesedwa colowa cace, popeza tinakonzekeratu monga mwa citsimikizo mtima ca iye wakucita zonse monga mwa uphungu wa cifuniro cace;
12 kuti ife amene dnakhulupirira Kristu kale tikayamikitse ulemerero wace.