4 koma Mulungu, wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru cimene anatikonda naco,
5 tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu (muli opulumutsidwa ndi cisomo),
6 ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Kristu Yesu;
7 kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Kristu Yesu.
8 Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu;
9 cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense.
10 Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.