13 Kristu anatiombola ku temberero la cilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa,Wotembereredwa ali yense woo paeikidwa pamtengo;
14 kutidalitso la Abrahamu mwa Yesu Kristu, licitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa cikhulupiriro.
15 Abale, ndinena monga munthu Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesacabe, kapena kuonjezapo.
16 Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace, Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Kristu.
17 Ndipo ici ndinena; Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lacabe.
18 Pakuti ngati kulowa nyumba kucokera kulamulo, sikucokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.
19 Nanga cilamulo tsono? Cinaoniezeka cifukwa ca zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo cinakonzeka ndi angelo m'dzanja la Ilkhoswe.