17 Ndipo ici ndinena; Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lacabe.
18 Pakuti ngati kulowa nyumba kucokera kulamulo, sikucokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.
19 Nanga cilamulo tsono? Cinaoniezeka cifukwa ca zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo cinakonzeka ndi angelo m'dzanja la Ilkhoswe.
20 Koma nkhoswe siiri ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi.
21 Pamenepo kodi cilamulo citsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti cikadapatsidwa cilamulo eakukhoza kucitira moyo, cilungamo cikadacokera ndithu kulamulo.
22 Komatu lembo Iinatsekereza zonse pansi pa ucimo, kuti lonjezano la kwa cikhulupiriro ca Yesu Kristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.
23 Koma cisanadze cikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira cikhulupiriro cimene cikabvumbulutsidwa bwino bwino.