10 Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakubvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza citsutso cace.
11 Koma ine, abale, ngati ndilalikiransoindulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo cikhumudwitso ca mtanda cidatha.
12 Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.
13 Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; cokhaco musacite nao ufulu wanu cothandizira thupi, komatu mwa cikondi citiranani ukapolo.
14 Pakuti mau amodzi akwaniritsa cilamulo conse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
15 Koma ngati mulumana ndi kudyana, cenjerani mungaonongane.
16 Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.