7 Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta.
8 Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, cocokera m'thupi adzatuta cibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, cocokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.
9 Koma tisaleme pakucita zabwino pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.
10 Cifukwa cace, monga tiri nayo nyengo, ticitire onse cokoma, koma makamaka iwo a pa banja la cikhulupiriro.
11 Taonani, malembedwe akuruwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini.
12 Onseamene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukangamizani inu mudulidwe; cokhaco, cakuti angazunzike cifukwa ca mtanda wa Kristu.
13 Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu.