Ezara 4 BL92

Asamariya aneneza Ayuda omanga Kacisi kwa Ahaswero

1 Atamva tsono a adani Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israyeli Kacisi,

2 anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe ciyambire masiku a Ezaradoni mfumu ya Asuri, amene anatikweretsa kuno.

3 Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akuru otsala a nyumba za makolo a Israyeli, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israyeli, monga mfumu Koresi mfumu ya Perisiya watilamulira.

4 Pamenepo anthu a m'dziko anafoketsa manja a anthu Ayuda, nawabvuta pomanga,

5 nalembera opangira atsutsane nao, nafafanize uphungu wao, masiku onse a Koresi mfumu ya Perisiya, mpaka ufumu wa Dariyo mfumu ya Perisiya.

6 Ndipo pokhala mfumu Ahaswero, poyambira ufumu wace, analembera cowaneneza okhala m'Yuda ndi m'Yerusalemu.

7 Ndipo masiku a Aritasasta Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli, ndi anzao otsala, analembera kwa Aritasasta mfumu ya Perisiya; ndi cilembedwe cace ca kalatayo anamlemba m'Ciaramu, namsanduliza m'Ciaramu.

8 Rehumu ciwinda ca malamulo, ndi Simsai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Aritasasta, wakutsutsana naye Yerusalemu motere:

9 nalembera Rehumu ciwinda ca malamulo, ndi Simsai mlembi, ndi anzace otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Arekavai, Ababulo, Asusanekai, Adehai, Aelimai,

10 ndi amitundu otsala amene, Osinapera wamkuru ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m'mudzi wa Samariya, ndi m'dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Firate, pa nthawi yakuti.

11 Zolembedwa m'kalatayo anamtumiza kwa Aritasasta mfumu ndizo: Akapolo anu, anthu a tsidya lino la mtsinjewo, ndi pa nthawi yakuti.

12 Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ocokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mudzi uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ace, nalumikiza maziko ace.

13 Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mudzi uwu ndi kutsiriza malinga ace, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pace kudzasowetsa mafumu.

14 Popeza tsono timadya mcere wa m'nyumba ya mfumu, sitiyenera kungopenyerera mpepulo wa pa mfumu; cifukwa cace tatumiza ndi kudziwitsa mfumu,

15 kuti afunefune m'buku la cikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la cikumbutso, ndi kudziwa kuti mudzi uwu ndi mudzi wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndico cifukwa cakuti anapasula mudzi uwu.

16 Tirikudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mudziwu, nakatsirizidwa malinga ace, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.

Mfumu iwaletsa asamange Kacisi

17 Mfumu nibweza mau kwa Rehumu ciwinda ca malamulo, ndi kwa Simsai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala m'Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Mtendere, ndi nthawi yakuti.

18 Kalatayo mwatitumizira anandiwerengera momveka.

19 Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mudzi uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe ndi kuti akacitamo mpanduko ndi kudziyendera.

20 Panalinso mafumu amphamvu m'Yerusalemu amene anacita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.

21 Mulamulire tsono kuti anthu awa aleke, ndi kuti asamange mudzi uwu, mpaka ndidzalamulira ndine.

22 Cenjerani mungadodomepo, cidzakuliranji cisauko ca kusowetsa mafumu?

23 Pamenepo atawerenga malemba a kalata wa mfumu kwa Rehumu, ndi Simsai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu.

24 Momwemo inalekeka nchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka caka caciwiri ca ufumu wa Dariyo mfumu ya Perisiya.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10