Ezara 2 BL92

Maina a Ayuda obwera ku Yerusalemu ndi Zerubabele

1 Ana a deralo, amene anakwera kuturuka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babulo adawatenga ndende kumka nao ku Babulo, nabwerera kumka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense ku mudzi wace, ndi awa:

2 ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Moredekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israyeli ndiko:

3 ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

4 Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

5 Ana a Ara, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu.

6 Ana a Pahati Moabu, a ana a Yesuwa ndi Yoabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi awiri.

7 Ana a Elamu, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

8 Ana a Zatu, mazana asanu ndi anai mphambu makumi anai kudza asanu.

9 Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

10 Ana a Bani, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.

11 Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

12 Ana a Asigadi, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi awiri ndi awiri.

13 Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi.

14 Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi.

15 Ana a Adini, mazana anai mphambu makumi asanu kudza anai.

16 Ana a Ateri, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi atatu.

17 Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza atatu.

18 Ana a Yora, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.

19 Ana a Hasumu, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.

20 Ana a Gibara, makumi asanu ndi anai mphambu asanu.

21 Ana a Betelehemu zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.

22 Anthu a ku Netofa, makumi asanu mphambu asanu ndi mmodzi.

23 Anthu a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

24 Ana a Azimaveti, makumi anai mphambu awiri.

25 Ana a Kiriyati Arimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu.

26 Ana a Rama ndi Gaba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

27 Anthu a Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

28 Anthu a ku Beteli ndi Ai, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.

29 Ana a Nebo, makumi asanu mphambu awiri.

30 Ana a Magabisi, zana limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi.

31 Ana a Elamu wina, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

32 Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.

33 Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza asanu.

34 Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.

35 Ana a Senai, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.

36 Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.

37 Ana a lmneri, cikwi cimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

38 Ana a Pasuru, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.

39 Ana a Harimu, cikwi cimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri.

40 Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyeli, ndiwo a ana a Hodariya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai.

41 Oyimba: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

42 Ana a odikira: ana a Sabumu, ana a Ateri, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, onse pamodzi ndiwo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi anai.

43 Anetini: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,

44 ana a Kerosi, ana a Siaha, ana a Padoni,

45 ana a Lebano, ana a Hagaba, ana a Akubu,

46 ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani,

47 ana a Gideli, ana a Gahari, ana a Reaya,

48 ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu,

49 ana a Uza, ana a Paseya, ana a Besai,

50 ana a Asina, ana a Mehunimu, ana a Nefusimu,

51 ana a Bakabuku, ana a Hakufa, ana a Haruri,

52 ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa,

53 ana a Barikosi, ana a Siseri, ana a Tama,

54 ana a Neziya, ana a Hatifa.

55 Ana a akapolo a Solomo: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,

56 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,

57 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti wa Zebaimu, ana a Ami.

58 Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomo, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.

59 Ndipo okwera kucokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adana, Imeri, ndi awa, koma sanakhoza kuchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisrayeli:

60 ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

61 Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Kozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgileadi, nachedwa dzina lao.

62 Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa cibadwidwe cao, koma osawapeza; potero anacotsedwa ku nchito ya nsembe monga odetsedwa.

63 Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulikitsa, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.

64 Msonkhano wonse pamodzi ndiwo wa zikwi makumi anai ndi awiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,

65 osawerenga akapolo ao amuna ndi akazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao amuna ndi akazi oyimbira mazana awiri.

66 Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu;

67 ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; aburu zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.

68 Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika ku nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu, anapereka caufulu kwa nyumba ya Mulungu cakulimika pakuzika pace.

69 Monga momwe anakhoza anapereka ku cuma ca nchitoyi madariki agolidi: zikwi zisanu ndi cimodzi, miyeso ya siliva zikwi zisanu, ndi maraya a ansembe zana limodzi.

70 Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oyimbira, ndi odikira, ndi Anetini, anakhala m'midzi mwao, ndi Aisrayeli onse m'midzi mwao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10