1 Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala m'Yuda ndi m'Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israyeli ananenera kwa iwo.
2 Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.
3 Nthawi yomweyi anawadzera Tatinai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setara Bozinai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?
4 Nanena naonso motere, Maina ao a anthu omanga cimangidwe ici ndiwo ayani?
5 Koma diso la Mulungu wao linali pa akuru a Ayuda, ndipo sanawaletsa mpaka mlandu unamdzera Dariyo, nabweza mau a mlanduwo m'kalata.
6 Zolembedwa m'kalata amene Tatinai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setara Bozenai, ndi anzace Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariyo mfumu,
7 anatumiza kalata kwa iyeyo m'menemo munalembedwa motere, Kwa Dariyo mfumu, mtendere wonse.
8 Adziwe mfumu kuti ife tinamuka ku dziko la Yuda, ku nyumba ya Mulungu wamkuru, yomangidwa ndi miyala yaikuru, niikidwa mitengo pamakoma, nicitika mofulumira nchitoyi, nikula m'dzanja mwao.
9 Pamenepo tinafunsa akulu aja ndi kutere nao, Anakulamulirani ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?
10 Tinawafunsanso maina ao, kukudziwitsani, kuti tilembere maina a anthu akuwatsogolera.
11 Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa Kumwamba ndi dziko lapansi, tirikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikuru ya Israyeli.
12 Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo Mkasidi, amene anaononga nyumba yino, natenga anthu ndende kumka nao ku Babulo.
13 Koma caka coyamba ca Koresi mfumu ya Babulo, Koresi mfumuyo analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu.
14 Ndiponso zipangizo za golidi ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anaziturutsa Nebukadinezara m'Kacisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku kacisi wa ku Babulo, izizo Koresi mfumu anaziturutsa m'kacisi wa ku Babulo, nazipereka kwa munthu dzina lace Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;
15 nati naye, Tenga zipangizo izi, kaziike m'Kacisi ali m'Yerusalemu, nimangidwe nyumba ya Mulungu pambuto pace.
16 Pamenepo anadza Sezibazara yemweyo namanga maziko a nyumba ya Mulungu iri m'Yerusalemu; ndipo kuyambira pomwepo kufikira tsopano irimkumangidwa, koma siinatsirizike.
17 Ndipo tsono cikakomera mfumu, munthu asanthule m'nyumba ya cuma ca mfumu iri komwe ku Babulo, ngati nkuterodi, kuti Koresi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa cinthuci.