Ezara 8 BL92

Maina a opita ndi Ezara. Ulendo wao mpaka Yerusalemu

1 Ndipo akuru a nyumba za makolo ndi awa, ndi cibadwidwe ca iwo okwera nane limodzi kucokera ku Babulo, pokhala mfumu Aritasasta, ndi ici:

2 wa ana a Pinehasi, Gerisomu; wa ana a Itamara, Danieli; wa ana a Davide, Hatusi.

3 Wa ana a Sekaniya, wa ana a Parosi, Zekariya; ndi pamodzi naye, powawerenga monga mwa cibadwidwe cao, amuna zana limodzi mphambu makumi asanu.

4 Wa ana a Pahati Moabu, Elihoenai mwana wa Zerahiya; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri.

5 Wa ana a Sekaniya, mwana wa Yahazieli; ndi pamodzi naye amuna mazana atatu.

6 Ndi wa ana a Adini, Ebedi mwana wa Yonatani; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu.

7 Ndi wa ana a Elamu, Yesaya mwana wa Ataliya; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi awiri.

8 Ndi wa ana a Sefatiya, Zebadiya mwana wa Mikaeli; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi atatu.

9 Wa ana a Yoabu, Obadiya mwana wa Yehieli; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri mphambu khumi kudza asanu ndi atatu.

10 Ndi wa ana a Selomiti, mwana wa Yosifiya; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi.

11 Ndi wa ana a Bebai, Zekariya mwana wa Bebai; ndi pamodzi naye amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu.

12 Ndi wa ana a Azigadi, Yohanana mwana wa Hakatana; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu khumi limodzi.

13 Ndi a ana otsiriza a Adonikmnu, maina ao ndiwo Elifeleti, Yeueli, ndi Semaya; ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi limodzi.

14 Ndi wa ana a Bigivai, Utai ndi Zabudi, ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi awiri.

15 Ndipo ndinawasonkhanitsa ku mtsinje wopita ku Ahava, ndi komweko tinakhala m'misasa masiku atatu; ndipo ndinapenyerera anthu ndi ansembe, koma sindinapezapo wa ana a Levi.

16 Pamenepo ndinatumiza munthu kuitana Eliezere, Ariyeli, Semaya, ndi Elimatana, ndi Natani, ndi Zekariya, ndi Mesulamu, ndiwo akuru; ndi Yoyaribi ndi Elinatani, ndiwo aphunzitsi.

17 Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkuru, ku malo dzina lace Kasifiya; ndinalooganso m'kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ace Anetini, pa malo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu.

18 Ndipo monga munatikhalira dzanja lokoma la Mulungu wathu, anatitengera munthu wanzeru wa ana a Mali, mwana wa Levi, mwana wa Israyeli; ndi Serebiya, pamodzi ndi ana ace ndi abale ace khumi mphambu asanu ndi atatu;

19 ndi Hasabiya, ndi pamodzi naye Yesaya wa ana a Merari, abale ace ndi ana ao makumi awiri;

20 ndi a Anetini, amene Davide ndi akalonga adapereka atumikire Alevi, Anetini mazana awiri mphambu makumi awiri, onsewo ochulidwa maina.

21 Pamenepo ndinalalikira cosala komweko ku mtsinje wa Ahava, kuti tidzicepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang'ono athu, ndi cuma cathu conse.

22 Pakuti ndinacita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikari, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yace ndi mkwiyo wace zitsutsana nao onse akumsiya.

23 Momwemo tinasala ndi kupempha ici kwa Mulungu wathu; natibvomereza Iye,

24 Pamenepo ndinapatula akulu a ansembe khumi ndi awiri, ndiwo Serebiya, Hasabiya, ndi abale ao khumi pamodzi nao,

25 ndi kuwayesera siliva, ndi golidi, ndi zipangizo, ndizo copereka ca kwa nyumba ya Mulungu wathu, cimene mfumu, ndi aphungu ace, ndi akalonga ace, ndi Aisrayeli onse anali apawa, adapereka.

26 Ndipo ndinawayesera m'dzanja mwao matalente a siliva mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu, ndi zipangizo zasiliva matalente zana limodzi,

27 ndi zikho zagolidi makumi awiri za madariki cikwi cimodzi, ndi zipangizo ziwiri za mkuwa wabwino wonyezimira wokhumbika ngati golidi.

28 Ndipo ndinanena nao, Inu ndinu opatulikira Yehova, ndi zipangizozo nzopatulikira, ndi siliva ndi golidi, ndizo copereka caufulu ca kwa Yehova Mulungu wa makolo anu.

29 Mukhale maso ndi kuzisunga mpaka muziyesera pamaso pa akulu a ansembe ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo a Israyeli ku Yerusalemu, m'zipinda za nyumba ya Yehova.

30 Potero ansembe ndi Alevi analandira kulemera kwace kwa siliva ndi golidi ndi zipangizo, abwere nazo ku Yerusalemu ku nyumba ya Mulungu wathu.

31 Pamenepo tinacoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi ciwiri la mwezi woyamba, kumka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira.

32 Ndipo tinafika ku Yerusalemu ndi kukhalako masiku atatu.

33 Ndi pa tsiku lacinai siliva ndi golidi ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uliya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Pinehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadia mwana wa Binui, Alevi;

34 zonsezi anaziwerenga ndi kuziyesa; ndi kulemera kwace konse kunalembedwa nthawi yomweyo.

35 Otengedwa ndende, ataturuka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israyeli, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisrayeli onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, ana a nkhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.

36 Ndipo anapereka malamulo a mfumu kwa akazembe a mfumu, ndi kwa ziwanga, tsidya lino la mtsinjewo; ndipo iwo anathandiza anthu ndi nyumba ya Mulungu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10