1 Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Aritasasta mfumu ya Perisiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
2 mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubu,
3 mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Meraioti,
4 mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki,
5 mwana wa Abisuwa mwana wa Pinehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkuru.
6 Ezara amene anakwera kucokera ku Babulo, ndiye mlembi waluntha m'cilamulo ca Mose, cimene Yehova Mulungu wa Israyeli adacipereka; ndipo mfumu inampatsa copempha iye conse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wace.
7 Nakweranso kumka ku Yerusalemu ena a ana a Israyeli, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oyimbira, ndi odikira, ndi Anetini, caka cacisanu ndi ciwiri ca Aritasasta mfumu.
8 Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wacisanu, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca mfumu.
9 Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo ciyambi ca ulendo wokwera kucokera ku Babulo, ndi tsiku lacimodzi la mwezi wacisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wace.
10 Pakuti Ezara adaikiratu mtima wace kucifuna cilamulo ca Yehova, ndi kucicita, ndi kuphunzitsa m'Israyeli malemba ndi maweruzo.
11 Malemba a kalatayo mfumu Aritasasta anampatsa Ezara wansembe mlembi, ndiye mlembi wa mau a malamulo a Yehova, ndi malemba ace kwa Israyeli, ndi awa:
12 Aritasasta mfumu ya mafumu kwa Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, mtendere weni weni, ndi pa nthawi yakuti.
13 Ndilamulira kuti onse a ana a Israyeli, ndi ansembe ao, ndi Alevi, m'ufumu wanga, ofuna eni ace kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.
14 Popeza utumidwa wocokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ace asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako liri m'dzanja lako,
15 ndi kumuka nazo siliva ndi golidi, zimene mfumu ndi aphungu ace, anapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Israyeli, mokhala mwace muli m'Yerusalemu,
16 pamodzi ndi siliva ndi golidi ziri zonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babulo, pamodzi ndi copereka caufulu ca anthu, ndi ca ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao iri ku Yerusalemu;
17 m'mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng'ombe, nkhosa zamphongo, ana a nkhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka pa guwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu.
18 Ndipo ciri conse cidzakomera iwe ndi abale ako kucita nazo siliva ndi golidi zotsala, ici mucite monga mwa cifuniro ca Mulungu wanu.
19 Ndipo zipangizozo akupatsa za utumiki wa nyumba ya Mulungu wako, uzipereka pamaso pa Mulungu wa ku Yerusalemu.
20 Ndi zina zotsala zakusowa nyumba ya Mulungu wako, zikayenera uzipereke, uzipereke zocokera ku nyumba ya cuma ca mfumu.
21 Ndipo ine Aritasasta, mfumu ine, ndilamulira osunga cuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti ciri conse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, cicitike mofulumira;
22 mpaka matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zana limodzi, ndi miyeso ya vinyo zana limodzi, ndi miyeso ya mafuta zana limodzi, ndi mcere wosauwerenga.
23 Ciri conse Mulungu wa Kumwamba acilamulire cicitikire mwacangu nyumba ya Mulungu wa Kumwamba; pakuti padzakhaliranji mkwiyo pa ufumu wa mfumu ndi ana ace?
24 Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa ali yense wa ansembe, ndi Alevi, oyimbira, odikira, Anetini, kapena anchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.
25 Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako iri m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza mirandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.
26 Ndipo ali yense wosacita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpitikitsa m'dziko, kapena kumlanda cuma cace, kapena kummanga m'kaidi.
27 Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika cinthu cotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu,
28 nandifikitsira cifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ace, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israyeli anthu omveka akwere nane limodzi.