1 Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israyeli msonkhano waukuru ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira, kwakukuru.
2 Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyeli, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi acilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano cimtsalira Israyeli ciyembekezo kunena za cinthu ici.
3 Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kucotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo cicitike monga mwa cilamulo.
4 Nyamukani, mlandu ndi wanu; ndipo ife tiri nanu; limbikani, citani.
5 Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisrayeli onse, kuti adzacita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo.
6 Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya. Mulungu, nalowa m'cipinda ca Yehohanana mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadya mkate, sanamwa madzi; pakuti anacita maliro cifukwa ca kulakwa kwa iwo otengedwa ndende.
7 Nabukitsa iwo mau mwa Yuda ndi Yerusalemu kwa ana onse otengedwa ndende, kuti azisonkhana ku Yerusalemu;
8 ndi kuti ali yense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akuru, cuma cace conse cidzaonongeka konse, ndipo iye adzacotsedwa ku msonkhano wa iwo otengedwa ndende.
9 Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wacisanu ndi cinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera cifukwa ca mlandu uwu, ndi cifukwa ca mvulayi.
10 Pamenepo Ezara wansembe ananyamuka, nanena nao, Mwalakwa, mwadzitengera akazi acilendo, kuonjezera kuparamula kwa Israyeli.
11 Cifukwa cace tsono, ululani kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, nimucite comkondweretsa; mudzilekanitse ndi mitundu ya anthu a m'dzikomo, ndi kwa akazi acilendo.
12 Ndipo unayankha msonkhano wonse, ndi kunena ndi mau akuru, Monga mwa mau anu tiyenera kucita.
13 Koma anthu ndiwo ambiri, ndi nyengo yino nja mvula, tiribenso mphamvu yakuima pabwalo, ndi nchitoyi sindiyo ya tsiku limodzi kapena awiri; pakuti tacurukitsa kulakwa kwathu pa cinthu ici.
14 Ayang'anire ici tsono akalonga athu a msonkhano wonse, ndi onse a m'midzi mwathu amene anadzitengera akazi acilendo abwere pa nthawi zoikika, ndi pamodzi nao akuru a mudzi wao uli wonse, ndi oweruza ace, mpaka udzaticokera mkwiyo waukali wa Mulungu wathu cifukwa ca mlandu uwu.
15 Yonatani mwana wa Asaheli ndi Yazeya mwana wa Tikiva okha anatsutsana naco, ndi Mesulamu ndi Sabetai Mlevi anawathandiza.
16 Pamenepo anthu otengedwa ndende anacita cotero. Ndi Ezara wansembe, ndi anthu akuru a nyumba za makolo, monga mwa nyumba za makolo ao, iwo onse ochulidwa maina ao anasankhidwa, nakhala pansi tsiku loyamba la mwezi wakhumi kufunsa za mlanduwu.
17 Natsiriza nao amuna onse adadzitengera akazi acilendo tsiku loyamba la mwezi woyamba.
18 Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi acilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ace Maseya, ndi Eliezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya.
19 Ndipo anaimika dzanja lao kuti adzacotsa akazi ao; ndipo popeza adaparamuladi, anapereka nsembe nkhosa yamphongo ya zoweta pa kuparamula kwao.
20 Ndi a ana a Imeri: Hanani ndi Zebadiya.
21 Ndi a ana a Harimu: Maseya, ndi Eliya, ndi Semaya, ndi Yehiyeli, ndi Uziya.
22 Ndi a ana a Pasuru: Elioenai, Maseya, Ismayeli, Netaneli, Yozabadi, ndi. Elasa.
23 Ndi a Alevi: Yozabadi, ndi Simei, ndi Kelaya (ndiye Kelita), Petahiya, Yuda, ndi Eliezere.
24 Ndi a oyimbira: Eliasibu; ndi a odikira: Salumu, ndi Telemu, ndi Uri.
25 Ndi Aisrayeli a ana a Parosi: Ramiya, ndi Iziya, ndi Matikiya, ndi Miyamini, ndi Eleazara, ndi Malikiya, ndi Benaya.
26 Ndi a ana a Elamu: Mataniya, Zekariya, ndi Yehieli, ndi Abidi, ndi Yeremoti, ndi Eliya.
27 Ndi a ana a Zatu: Elioenai, Eliasibi, Mataniya, ndi Yeremoti, ndi Zabadi, ndi Aziza.
28 Ndi a ana a Bebai: Yehohanana, Hananiya, Zabai, Atilai.
29 Ndi a ana a Bani: Mesulamu, Makuli, ndi Adaya, Yasubi, ndi Seali, Yeremoti.
30 Ndi a ana a Pahati: Moabu, Adina, ndi Kelali, Benaya, Maseya, Mataniya, Bezaleli, ndi Binui, ndi Manase.
31 Ndi a ana a Harimu: Eliezere, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni,
32 Benjamini, Maluki, Semariya.
33 A ana a Hasumu: Matenai, Matata. Zabadi, Elifeleti, Yeremai, Manase, Simei.
34 A ana a Bani: Madai, Amiramu, ndi Ueli,
35 Benaya, Bedeya, Kelui,
36 Vaniya, Meremoti, Eliasibi,
37 Mataniya, Matenai, ndi Yasu,
38 ndi Bani, ndi Binui, Simei,
39 ndi Selemiya, ndi Natani, ndi Adaya,
40 Makinadebai, Sasai, Sarai,
41 Azareli, ndi Seleimiya, Semariya,
42 Salumu, Amariya, Yosefe.
43 A ana a Nebo: Yeieli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Ido, ndi Yoeli, Banaya,
44 Awa onse adatenga akazi acilendo, ndi ena a iwowa anali ndi akazi amene adawabalira ana.