Ezara 6 BL92

Dariyo anenetsa kuti Kacisi amangidwe

1 Pamenepo analamulira Dariyo mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira cuma m'Babulo.

2 Napeza ku Akimeta m'nyumba ya mfumu m'dera la Mediya, mpukutu, ndi m'menemo munalembedwa motere, cikhale cikumbutso:

3 Caka coyamba ca Koresi mfumu, analamulira Koresi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ace, msinkhu wace mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwace mikono makumi asanu ndi limodzi;

4 ndi mipambo itatu ya miyala yaikuru, ndi mpambo wa mitengo yatsopano; nalipidwe ndarama zocokera ku nyumba ya mfumu.

5 Ndi zipangizo za golidi ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anaziturutsa Nebukadinezara m'Kacisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kumka nazo ku Babulo, azibwezere, nabwere nazo ku Kacisi ali ku Yerusalemu, ciri conse ku malo ace; naziike m'nyumba ya Mulungu.

6 Tsono iwe, Tatinai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setara Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;

7 lekani nchito iyi ya Mulungu, osaibvuta; kazembe wa Ayuda ndi akulu a Ayuda amange nyumba iyi ya Mulungu pambuto pace.

8 Ndilamuliranso za ici muzicitira akuru awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko cuma ca mfumu, ndico msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawacedwetse.

9 Ndipo zosowa zao, ana a ng'ombe, ndi nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa, zikhale nsembe zopsereza za Mulungu wa Kumwamba; tirigu, mcere, vinyo, mafuta, monga umo adzanena ansembe ali ku Yerusalemu, ziperekedwe kwa iwo tsiku ndi tsiku, zisasoweke;

10 kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ace.

11 Ndalamuliranso kuti ali yense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwace, namkweze, nampacike pomwepo; niyesedwe dzala nyumba yace cifukwa ca ici;

12 ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lace komweko agwetse mafwnu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akuturutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndalamulira, cicitike msanga.

13 Pamenepo Tatinai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setara Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariyo adatumiza mau, anacita momwemo cofulumira.

14 Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda cosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israyeli, ndi monga mwa lamulo la Koresi, ndi Dariyo, ndi Aritasasta mfumu ya Perisiya,

15 Nitsirizidwa nyumba iyi tsiku lacitatu la mwezi wa Adara, ndico caka cacisanu ndi cimodzi ca ufumu wa Dariyo mfumu.

Apereka Kacisi nacita Paskha

16 Ndipo ana a Israyeli, ansembe ndi Alevi, ndi ana otsala a ndende, anapereka nyumba iyi ya Mulungu mokondwera.

17 Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng'ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, ana a nkhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisrayeli onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwace kwa mapfuko a Israyeli.

18 Naika ansembe m'magawo mwao, ndi Alevi m'magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m'buku la Mose.

19 Ndipo ana a ndende anacita Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi woyamba.

20 Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paskha cifukwa ca ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha.

21 Ndipo ana a Israyeli obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kucokera conyansa ca amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, anadza,

22 nasunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asuri, kulimbitsa manja ao mu nchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10