1 Atamva tsono a adani Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israyeli Kacisi,
2 anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe ciyambire masiku a Ezaradoni mfumu ya Asuri, amene anatikweretsa kuno.
3 Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akuru otsala a nyumba za makolo a Israyeli, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israyeli, monga mfumu Koresi mfumu ya Perisiya watilamulira.
4 Pamenepo anthu a m'dziko anafoketsa manja a anthu Ayuda, nawabvuta pomanga,
5 nalembera opangira atsutsane nao, nafafanize uphungu wao, masiku onse a Koresi mfumu ya Perisiya, mpaka ufumu wa Dariyo mfumu ya Perisiya.