2 Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.
3 Nthawi yomweyi anawadzera Tatinai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setara Bozinai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?
4 Nanena naonso motere, Maina ao a anthu omanga cimangidwe ici ndiwo ayani?
5 Koma diso la Mulungu wao linali pa akuru a Ayuda, ndipo sanawaletsa mpaka mlandu unamdzera Dariyo, nabweza mau a mlanduwo m'kalata.
6 Zolembedwa m'kalata amene Tatinai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setara Bozenai, ndi anzace Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariyo mfumu,
7 anatumiza kalata kwa iyeyo m'menemo munalembedwa motere, Kwa Dariyo mfumu, mtendere wonse.
8 Adziwe mfumu kuti ife tinamuka ku dziko la Yuda, ku nyumba ya Mulungu wamkuru, yomangidwa ndi miyala yaikuru, niikidwa mitengo pamakoma, nicitika mofulumira nchitoyi, nikula m'dzanja mwao.