1 Pamenepo analamulira Dariyo mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira cuma m'Babulo.
2 Napeza ku Akimeta m'nyumba ya mfumu m'dera la Mediya, mpukutu, ndi m'menemo munalembedwa motere, cikhale cikumbutso:
3 Caka coyamba ca Koresi mfumu, analamulira Koresi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ace, msinkhu wace mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwace mikono makumi asanu ndi limodzi;
4 ndi mipambo itatu ya miyala yaikuru, ndi mpambo wa mitengo yatsopano; nalipidwe ndarama zocokera ku nyumba ya mfumu.
5 Ndi zipangizo za golidi ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anaziturutsa Nebukadinezara m'Kacisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kumka nazo ku Babulo, azibwezere, nabwere nazo ku Kacisi ali ku Yerusalemu, ciri conse ku malo ace; naziike m'nyumba ya Mulungu.
6 Tsono iwe, Tatinai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setara Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;