7 lekani nchito iyi ya Mulungu, osaibvuta; kazembe wa Ayuda ndi akulu a Ayuda amange nyumba iyi ya Mulungu pambuto pace.
8 Ndilamuliranso za ici muzicitira akuru awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko cuma ca mfumu, ndico msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawacedwetse.
9 Ndipo zosowa zao, ana a ng'ombe, ndi nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa, zikhale nsembe zopsereza za Mulungu wa Kumwamba; tirigu, mcere, vinyo, mafuta, monga umo adzanena ansembe ali ku Yerusalemu, ziperekedwe kwa iwo tsiku ndi tsiku, zisasoweke;
10 kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ace.
11 Ndalamuliranso kuti ali yense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwace, namkweze, nampacike pomwepo; niyesedwe dzala nyumba yace cifukwa ca ici;
12 ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lace komweko agwetse mafwnu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akuturutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndalamulira, cicitike msanga.
13 Pamenepo Tatinai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setara Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariyo adatumiza mau, anacita momwemo cofulumira.