1 Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israyeli, ndi ansembe, ndi Alevi, sanadzilekanitsa ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amoabu, Aaigupto, ndi Aamori.
2 Pakuti anadzitengera okha ndi ana amuna ao ana akazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.
3 Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba cobvala canga, ndi maraya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndebvu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.
4 Nandisonkhanira ali yense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israyeli, cifukwa ca kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.