Ezara 9:7-13 BL92

7 Ciyambire masiku a makolo athu taparamula kwakukuru mpaka lero lino; ndi cifukwa ca mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m'dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kucitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino.

8 Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa cisomo, kutisiyira cipulumutso, ndi kutipatsa ciciri m'malo mwace mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono m'ukapolo wathu.

9 Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiya m'ukapolo wathu, natifikitsira cifundo pamaso pa mafumu a Perisiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wace, ndi kutipatsa linga m'Yuda ndi m'Yerusalemu.

10 Ndipo tsopano, Mulungu wathu, tidzanenanji pambuyo pa ici? pakuti tasiya malamulo anu,

11 amene munalamulira mwa atumiki anu aneneri ndi kuti, Dzikolo mumukako likhale colowa canu ndilo dziko lodetsedwa mwa cidetso ca anthu a m'maikomo, mwa zonyansa zao zimene zinalidzaza, kuyambira nsonga yina kufikira nsonga inzace ndi ucisi wao.

12 Cifukwa cace tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthwawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu colowa ca ku nthawi yonse.

13 Ndipo zitatigwera zonsezi cifukwa ca nchito zathu zoipa ndi kuparamula kwathu kwakukuru; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga moticepsera mphulupulu zathu, ndi ku tipatsa cipulumutso cotere;