Hoseya 12 BL92

Mlandu wa Yehova pa Israyeli ndi Yuda

1 Efraimu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse acurukitsa mabodza ndi cipasuko, ndipo acita pangano ndi Asuri, natenga mafuta kumka nao ku Aigupto,

2 Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zace, adzambwezera monga mwa macitidwe ace.

3 M'mimba anagwira ku citende ca mkuru wace, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu;

4 inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Beteli, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;

5 ndiye Yehova Mulungu wa makamu, cikumbukilo cace ndi Yehova.

6 M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga cifundo ndi ciweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.

7 Ndiye Mkanani, m'dzanja lace muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa.

8 Ndipo Efraimu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera cuma m'nchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala cimo.

9 Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere dziko la Aigupto, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a masonkhano oikika.

10 Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndacurukitsa masomphenya; ndi pa dzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo.

11 Kodi Gileadi ndiye wopanda pace? akhala acabe konse; m'Giligala aphera nsembe yang'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'micera ya munda.

12 Ndipo Yakobo anathawira ku thengo la Aramu, ndi Israyeli anagwira nchito cifukwa ca mkazi, ndi cifukwa ca mkazi anaweta nkhosa.

13 Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israyeli kucokera m'Aigupto, ndi mwa mneneri anasungika.

14 Efraimu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wace, ndi Ambuye wace adzambwezera comtonza cace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14