Hoseya 5 BL92

Kulowerera kwa Israyeli

1 Imvani ici, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israyeli; cherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti ciweruzoci cinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabora.

2 Ndipo opandukawo analowadi m'zobvunda; koma Ine ndine wakuwadzudzula onsewo.

3 Ndimdziwa Efraimu, ndi Israyeli sandibisikira; pakuti Efraimu iwe, wacita citole tsopano, Israyeli wadetsedwa.

4 Macitidwe ao sawalola kubwerera kwa Mulungu wao; pakuti mzimu wacitole uli m'kati mwao, ndipo sadziwa Yehova.

5 Ndipo kudzikuza kwa Israyeli kudzamcitira umboni pamaso pace; cifukwa cace Israyeli ndi Efraimu adzakhumudwa m'mphulupulu mwao; Yudanso adzakhumudwa pamodzi nao.

6 Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikuru kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwacokera.

7 Anacita mosakhulupirika pa Yehova, pakuti anabala ana acilendo; mwezi wokhala udzawatha tsopano, pamodzi ndi maiko ao.

8 Ombani mphalasa m'Gibeya, ndi lipenga m'Rama; pfuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.

9 Efraimu adzasanduka bwinja tsiku lakudzudzula; mwa mapfuko a Israyeli ndadziwitsa codzacitikadi.

10 Akalonga a Yuda akunga anthu osuntha malire; ndidzawatsanulira mkwiyo wanga ngati madzi.

11 Efraimu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wace kutsata lamulolo.

12 Ndipo ndikhala kwa Efraimu ngati njenjete, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati cibvundi.

13 Pamene Efraimu anaona nthenda yace, ndi Yuda bala lace, Efraimu anamuka kwa Asuri, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuciritsani, kapena kupoletsa bala lanu.

14 Pakuti ndidzakhala kwa Efraimu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kucoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.

15 Ndidzamuka ndi kubwerera kumka kumalo kwanga, mpaka adzabvomereza kuparamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwacangu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14