Hoseya 11 BL92

Kusayamika kwa Israyeli; macenjezo ndi malonjezo

1 Pamene Israyeli anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali m'Aigupto.

2 Monga anawaitana, momwemo anawacokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema.

3 Koma Ine ndinaphunzitsa Efraimu kuyenda, ndinawafungata m'manja mwanga; koma sanadziwa kuti ndinawaciritsa.

4 Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za cikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira cakudya.

5 Iye sadzabwerera kumka ku dziko la Aigupto, koma Asuri adzakhala mfumu yace, popeza anakana kubwera.

6 Ndi lupanga lidzagwera midzi yace, lidzatha mipiringidzo yace, ndi kuononga cifukwa ca uphungu wao.

7 Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; cinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.

8 Ndidzakusiya bwanji, Efraimu? ndidzakupereka bwanji, Israyeli? ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zacifundo zanga zilira zonse pamodzi.

9 Sindidzacita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efraimu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi.

10 Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kucokera kumadzulo.

11 Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Aigupto, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asuri; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova.

12 Efraimu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israyeli ndi cinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14